Zimene Tingachite Poyamikira Mphatso Yaikulu Kwambiri Imene Mulungu Anatipatsa
1. N’chifukwa chiyani timayamikira kwambiri Yehova?
1 Pa ‘mphatso zabwino’ zonse zimene Yehova amatipatsa, dipo la Mwana wake ndi mphatso yaikulu kwambiri. (Yak. 1:17) Imatithandiza kupeza madalitso ambiri zedi, kuphatikizapo kukhululukidwa machimo athu. (Aef. 1:7) Chifukwa cha zimenezi, nthawi zonse timayamikira kwambiri Yehova chifukwa cha mphatso imeneyi. Timaganizira kwambiri za mphatso yapadera imeneyi makamaka panthawi ya Chikumbutso.
2. Kodi n’chiyani chingathandize ifeyo komanso anthu a m’banja lathu kuyamikira dipo?
2 Thandizani a M’banja Lanu Kuyamikira Kwambiri Dipo: Kuti muwathandize kuyamikira kwambiri mphatso imeneyi, kutatsala milungu yochepa kuti mufike pa March 30, lomwe ndi tsiku la Chikumbutso, mungachite bwino kukambirana mfundo zokhudza dipo panthawi ya Kulambira kwa Banja. Komanso muziwerengera pamodzi tsiku lililonse malemba amene asankhidwa kuti tiwerenge panyengo ya Chikumbutso. Ganizirani mmene dipo lakuthandizirani inuyo panokha ndiponso mmene lakhudzira mmene mumaonera Yehova. Ganiziraninso mmene dipo lakhudzira mmene mumadzionera nokha, mmene mumaonera anthu ena ndiponso mmene mumaonera tsogolo lanu. Zingakhalenso bwino kukonzekera nyimbo nambala 8 ndi 5 zomwe ndi nyimbo zatsopano zimene tiziimba pa Chikumbutso.—Sal. 77:12.
3. Kodi tingatani kuti tisonyeze kuti timayamikira dipo?
3 Zimene Tingachite Posonyeza Kuti Timayamikira Dipo: Kuyamikira dipo kumatilimbikitsa kuuza anthu ena za Yehova ndiponso za chikondi chake chachikulu chimene chinamuchititsa kutumiza Mwana wake. (Sal. 145:2-7) M’miyezi ya March, April, ndi May, mabanja ena amasonyeza kuyamikira kwawo dipo pokonza zoti mwina munthu mmodzi m’banjalo achite upainiya wothandiza. Ngati zimenezi sizingatheke m’banja lanu, mungachite bwino ‘kuwombola nthawi’ kuti muwonjezere zimene mumachita mu utumiki. (Aef. 5:16) Kuyamikira dipo kumatilimbikitsanso kuthandiza anthu ena kuti adzakhale nafe pa Chikumbutso. (Chiv. 22:17) Yambani kulemba maina a anthu amene mumapangako maulendo obwereza, amene mumaphunzira nawo Baibulo, achibale anu, anzanu akuntchito ndiponso oyandikana nawo nyumba. Ndiyeno, yesetsani kugwira nawo ntchito yapadera yogawira timapepala toitanira anthu ku Chikumbutso.
4. Kodi nyengo ya Chikumbutso tingaigwiritse ntchito bwanji mwanzeru?
4 Nyengo ya Chikumbutso imatipatsa mpata wosonyeza mmene timayamikirira mphatso imene Yehova anatipatsa. Tiyeni tigwiritse ntchito nthawi imeneyi poyamikira kwambiri dipo ndiponso “chuma chopanda polekezera cha Khristu.”—Aef. 3:8.