MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Khalani ndi Zolinga pa Nyengo ya Chikumbutso
Chaka chilichonse, anthu a Yehovafe timayembekezera kuchitira limodzi mwambo wa Chikumbutso. Chikumbutsocho chikatsala pang’ono kuchitika komanso pambuyo poti chachitika, timayesetsa kugwiritsa ntchito mwayi wapadera omwe timakhala nawo kuti titamande komanso kuthokoza Yehova chifukwa cha mphatso ya dipo. (Aef 1:3, 7) Mwachitsanzo timagwira nawo ndi mtima wonse ntchito yoitanira anthu ku mwambowu. Ena amakwanitsa kusintha zinthu zina pa moyo wawo n’cholinga choti achite upainiya wothandiza wa maola 30 kapena 50 m’mwezi wa March kapena April. Pa nyengo ya Chikumbutso ya chaka chino, kodi mungakonde mutawonjezera nthawi imene mumalalikira? N’chiyani chingakuthandizeni kuchita zimenezi?
Nthawi zambiri anthu timatha kuchita zambiri tikakonzekeratu. (Miy 21:5) Choncho popeza kuti nyengo ya Chikumbutso yayandikira, panopa ndi nthawi yabwino yoyamba kukonzekera. Ganizirani kuchuluka kwa nthawi yolalikira imene mungakonde kuwonjezera pa nyengo ya Chikumbutso kenako onani zimene mungachite kuti mukwanitse cholinga chanuchi. Mukatero pemphani Yehova kuti adalitse zimene mwasankhazo.—1Yo 5:14, 15.
Kodi mungaganizire njira zina zimene zingakuthandizeni kuchita zambiri mu utumiki pa nyengo ya Chikumbutsoyi?