Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w24 January tsamba 8-14
  • Kodi Mwakonzeka Kudzapezekapo pa Tsiku Lofunika Kwambiri pa Chaka?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mwakonzeka Kudzapezekapo pa Tsiku Lofunika Kwambiri pa Chaka?
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • KODI TINGAKONZEKERETSE BWANJI MTIMA WATHU PA NTHAWI YA CHIKUMBUTSO?
  • TIZITHANDIZA ENA KUTI ADZAPINDULE
  • MUDZATHANDIZE AMENE ANASIYA KUSONKHANA
  • Madalitso Amene Timapeza Chifukwa cha Chikondi cha Yehova
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
  • Kodi Dipo Limatiphunzitsa Chiyani?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
  • Yehova Amadalitsa Khama Lathu Loyesetsa Kuti Tipezeke pa Chikumbutso
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
  • Khalani ndi Zolinga pa Nyengo ya Chikumbutso
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
w24 January tsamba 8-14

NKHANI YOPHUNZIRA 2

NYIMBO NA. 19 Chakudya Chamadzulo cha Ambuye

Kodi Mwakonzeka Kudzapezekapo pa Tsiku Lofunika Kwambiri pa Chaka?

“Muzichita zimenezi pondikumbukira.”​—LUKA 22:19.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Tiona chifukwa chake tsiku la Chikumbutso lili lofunika kwambiri, mmene tingalikonzekerere komanso mmene tingathandizire ena kuti adzapezekepo.

1. N’chifukwa chiyani tsiku la Chikumbutso ndi lofunika kwambiri pa chaka? (Luka 22:19, 20)

KWA anthu a Yehova, tsiku lokumbukira imfa ya Khristu ndi lofunika kwambiri pa chaka. Ndi mwambo wokhawo umene Yesu analamula otsatira ake kuti aziuchita. (Werengani Luka 22:19, 20.) Timafunitsitsa kupezeka pamwambowu pa zifukwa zingapo. Tiyeni tikambirane zina mwa zifukwazi.

2. N’chifukwa chiyani timafunitsitsa kudzapezeka pa Chikumbutso?

2 Mwambo wa Chikumbutso umatithandiza kuti tiziganizira kufunika kwa dipo. Umatikumbutsa zimene tingachite posonyeza kuti timayamikira nsembe ya Yesu. (2 Akor. 5:14, 15) Timakhalanso ndi mwayi ‘wolimbikitsana’ ndi abale ndi alongo athu. (Aroma 1:12) Chaka chilichonse, abale ndi alongo ambiri omwe anasiya kusonkhana amapezeka pamwambowu. Ena amabwerera kwa Yehova chifukwa choona mmene abale ndi alongo anawalandirira. Ndipo anthu ambiri achidwi amayamba kuyenda pa njira yopita ku moyo chifukwa cha zimene aona komanso kumva pamwambowu. N’chifukwa chake timaona kuti mwambo wa Chikumbutso ndi wofunika kwambiri kwa ife.

3. Kodi Chikumbutso chimatithandiza bwanji kuti tikhale ogwirizana padziko lonse? (Onaninso chithunzi.)

3 Ganiziraninso mmene mwambo wa Chikumbutso umathandizira abale ndi alongo kukhala ogwirizana padziko lonse. Pa tsikuli dzuwa likamalowa, a Mboni za Yehova padziko lonse amakhala akuyamba kuchita mwambowu. Timamvetsera nkhani yomwe imafotokoza kufunika kwa dipo. Timayimba nyimbo ziwiri zotamanda Yehova, kuyendetsa zizindikiro ndiponso timayankha mochokera pansi pamtima kuti “ame” pa mapemphero 4 amene amaperekedwa. Pakamatha maola 24, mipingo yonse padziko lonse imakhala itachita zofanana. Taganizirani chisangalalo chimene Yehova ndi Yesu amakhala nacho akamaona tikuwalemekeza mogwirizana chonchi.

Zithunzi: Pa tsiku la Chikumbutso, abale ndi alongo m’mbali zosiyanasiyana za dzikoli akukonzekera kapena kuchita mwambo wapaderawu. 1. Ku Puerto Rico, banja likuonera pulogalamu yapadera ya Kulambira Kwa M’mawa. 2. Ku Italy, mwamuna ndi mkazi wake akulalikira ndipo akupatsa bambo wina kapepala komuitanira ku Chikumbutso. 3. Ku Kenya, abale awiri akuwerengera munthu lemba. 4. Ku Georgia, mayi ndi mwana wake wamkazi akupanga mkate wa pa Chikumbutso potsatira malangizo a muvidiyo yakuti “Mmene Mungapangire Mkate wa Chikumbutso.” 5. Ku India, abale ndi alongo akukonza mu Nyumba ya Ufumu komanso tebulo loti paikidwe zizindikiro. 6. Ku Thailand, m’bale akulandira bambo yemwe wafika ku Nyumba ya Ufumu. 7. Ku Japan, m’bale akupereka mbale ya mkate wopanda chofufumitsa kwa mlongo pa nthawi ya Chikumbutso.

Chikumbutso chimachititsa kuti tikhale ogwirizana padziko lonse (Onani ndime 3)f


4. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

4 Munkhaniyi tikambirana mafunso awa: Kodi tingatani kuti tikonzekeretse mtima wathu pa nthawi ya Chikumbutso? Kodi tingathandize bwanji ena kuti adzapindule ndi mwambowu? Komanso kodi tingathandize bwanji anthu omwe anasiya kusonkhana? Mayankho a mafunso amenewa atithandiza kuti tikonzekere bwino mwambo wofunika kwambiriwu.

KODI TINGAKONZEKERETSE BWANJI MTIMA WATHU PA NTHAWI YA CHIKUMBUTSO?

5. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kumaona kuti dipo ndi lamtengo wapatali? (Salimo 49:7, 8) (b) Kodi mwaphunzira chiyani mu vidiyo yakuti Kodi N’chifukwa Chiyani Yesu Anafa?

5 Njira yofunika kwambiri yomwe tingakonzekeretsere mtima wathu ndi kuganizira kufunika kwa nsembe ya Yesu Khristu. Patokha sitikanatha kudzipulumutsa ku uchimo ndi imfa. (Werengani Salimo 49:7, 8; onaninso vidiyo yakuti N’chifukwa Chiyani Yesu Anafa?)a Choncho pokonza zoti Yesu adzapereke moyo wake chifukwa cha ife, Yehova ndi Mwana wake wokondedwa anapereka mtengo wokwera kwambiri. (Aroma 6:23) Tikamaganizira kwambiri zimene Yehova ndi Yesu anatichitirazi, tingamayamikirenso kwambiri dipo. Tikambirana zinthu zingapo zovuta zimene Yehova ndi Yesu anachita kuti dipo liperekedwe. Koma choyamba, kodi dipo n’chiyani?

6. Kodi pankafunika chiyani kuti dipo liperekedwe?

6 Dipo ndi malipiro amene amaperekedwa pofuna kuwombola chinachake. Adamu, yemwe anali munthu woyambirira kulengedwa, anali wangwiro. Atachimwa, iye anataya mwayi wokhala ndi moyo wosatha. Iye sanataye moyo wake wokha, koma anatayanso wa ana ake onse. Kuti abwezeretse zimene Adamu anataya, Yesu anapereka nsembe moyo wake wangwiro. Pa nthawi yonse yomwe anali padzikoli, iye “sanachite tchimo ndipo sananenepo mawu achinyengo.” (1 Pet. 2:22) Pa nthawi ya imfa yake, Yesu anali wangwiro ngati mmene Adamu analili asanachimwe, choncho zinali zotheka kubwezeretsa moyo umene Adamu anataya.​—1 Akor. 15:45; 1 Tim. 2:6.

7. Kodi Yesu ali padzikoli anakumana ndi mayesero otani?

7 Yesu ali padzikoli anapitirizabe kumvera Atate wake wakumwamba ngakhale pamene ankakumana ndi mayesero ambiri. Ali mwana, iye ankafunika kumvera makolo ake omwe sanali angwiro ngakhale kuti iye anali wangwiro. (Luka 2:51) Ali mnyamata, iye ankafunika kupewa zinthu zimene zikanachititsa kuti asamvere makolo ake kapenanso kuti asakhale wokhulupirika kwa Yehova. Ndipo atakula, ankafunika kukana mayesero a Satana Mdyerekezi kuphatikizaponso zimene ankamuuza kuti asakhale wokhulupirika kwa Mulungu. (Mat. 4:1-11) Satana ankayesetsa kuti Yesu achimwe n’cholinga choti alephere kupereka dipo.

8. Kodi ndi mayesero ena ati omwe Yesu anapirira?

8 Pa utumiki wake wapadzikoli, Yesu anapiriranso mayesero ena ambiri. Ankazunzidwa ndipo adani ake ambiri ankamuopseza kuti amupha. (Luka 4:28, 29; 13:31) Ankafunikanso kupirira zimene ophunzira ake ankalakwitsa. (Maliko 9:33, 34) Pamene ankaimbidwa mlandu anachitiridwa nkhanza komanso kunyozedwa. Kenako anaphedwa imfa yowawa komanso yochititsa manyazi. (Aheb. 12:1-3) Ankafunika kupirira mbali yomaliza ya mayesero ake payekha, popanda kuthandizidwa ndi Yehova.b​—Mat. 27:46.

9. Kodi timamva bwanji tikaganizira za nsembe imene Yesu anapereka? (1 Petulo 1:8)

9 Kunena zoona, Yesu anakumana ndi mavuto aakulu kuti apereke dipo. Kodi kuganizira mavuto amene Yesu anakumana nawo chifukwa chofunitsitsa kupereka moyo wake, sikukukuchititsani kuti muzimukonda kwambiri?​—Werengani 1 Petulo 1:8.

10. Kodi Yehova analolera kuchita chiyani kuti dipo liperekedwe?

10 Nanga bwanji ponena za Yehova? Kodi iye anasonyeza bwanji kudzimana pokonza zoti Yesu apereke dipo? Yehova ndi Yesu amakondana kwambiri ngati mmene zimakhalira pakati pa bambo ndi mwana wake. (Miy. 8:30) Ndiye tangoganizani mmene zinamukhudzira Yehova kuona Yesu akupirira mayesero ambiri ali padzikoli. Mosakayikira zinamupweteka kwambiri kuona Mwana wake akuchitiridwa nkhanza, kukanidwa komanso kuyesedwa.

11. Perekani chitsanzo chosonyeza mmene Yehova anamvera pamene Yesu ankaphedwa.

11 Kholo lililonse limene mwana wake anamwalira, limadziwa bwino chisoni chimene chimakhalapo chifukwa cha kuferedwako. Timakhulupirira kwambiri kuti akufa adzauka, koma zimenezi sizithetsa ululu umene timamva munthu amene timamukonda akamwalira. Chitsanzochi chikutithandiza kumvetsa mmene Yehova anamvera poona Mwana wake akuvutika komanso kufa pa tsiku limenelo mu 33 C.E.c​—Mat. 3:17.

12. Kodi tingachite chiyani Chikumbutso chisanafike?

12 Lisanafike tsiku la Chikumbutso, bwanji osakonza zoti muphunzire panokha kapena pa kulambira kwa pabanja nkhani zokhudza dipo? Mungagwiritse ntchito Buku la Mboni za Yehova Lofufuzira Nkhani kapena mabuku ena ofotokoza Baibulo kuti mudziwe zambiri pa nkhaniyi.d Muyeneranso kutsatira ndandanda yowerengera Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso yomwe ili mu kabuku ka Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu. Komanso pa tsiku la Chikumbutso, musadzaiwale kuonera pulogalamu yapadera ya Kulambira Kwa M’mawa. Ngati titakonzekeretsa mtima wathu pa tsiku la Chikumbutso, tidzathandizanso ena kuti apindule ndi mwambowu.​—Ezara 7:10.

Zothandiza Pofufuza

Mukamafufuza nkhani zokhudza dipo, yesani kupeza mayankho a mafunso awa:

  • N’chifukwa chiyani dipo linali lofunika? N’chifukwa chiyani Yehova sanangokhululukira Adamu ndi Hava?

  • N’chifukwa chiyani Yesu anali woyenerera kubwera padziko lapansi komanso kudzapulumutsa anthu?

  • Kodi ndi madalitso ati panopa omwe timapeza chifukwa cha dipo?

  • Kodi dipo lidzatithandiza bwanji m’tsogolo?

TIZITHANDIZA ENA KUTI ADZAPINDULE

13. Tchulani chinthu choyamba chomwe tingachite kuti tithandize ena kupindula ndi Chikumbutso?

13 Kodi tingathandize bwanji ena kuti adzapindule ndi mwambo wa Chikumbutso? Chinthu choyamba ndi kuwaitanira kumwambowu. Kuwonjezera pa anthu omwe timawalalikira nthawi zonse, tingalembenso mayina a anthu amene tikufuna kuwaitana. Anthuwa angaphatikizepo achibale athu, anzathu a kuntchito, a kusukulu ndi ena. Ngakhale zitakhala kuti tilibe timapepala tokwanira toitanira anthu ku Chikumbutso, tingathe kuwatumizira linki ya timapepala tapazipangizo zamakono. Mukhoza kudabwa ndi kuchuluka kwa anthu omwe angabwere.​—Mlal. 11:6.

14. Perekani chitsanzo chosonyeza kuti kuitanira munthu amene timamudziwa ku Chikumbutso n’kothandiza.

14 Tikapatsa anthu omwe timawadziwa timapepala towaitanira ku Chikumbutso, zingawalimbikitse kuti adzapezekepo. Tsiku lina, mlongo wina yemwe mwamuna wake si wa Mboni, anadabwa mwamunayo atamuuza mosangalala kuti apita nawo ku Chikumbutso. N’chifukwa chiyani mlongoyu anadabwa? Chifukwa kwa nthawi yaitali, iye ankalimbikitsa mwamuna wakeyo kuti akapezekepo koma sankapita. Ndiye n’chiyani chinamuchititsa kuti apite pa nthawiyi? Mwamunayo anamuuza kuti, “Ndalandira kapepala kondiitanira.” Iye anafotokoza kuti analandira kapepalako kwa mkulu wina yemwe ankadziwana naye. Chaka chimenecho komanso zaka zina zambiri, mwamunayo anakhala akupezeka pa Chikumbutso.

15. Kodi tizikumbukira chiyani tikamaitanira ena ku Chikumbutso?

15 Muzikumbukira kuti anthu amene mungawaitanire ku Chikumbutso angakhale ndi mafunso makamaka ngati n’koyamba kupezeka pamisonkhano yathu. Tingachite bwino kudziwiratu mafunso omwe angatifunse n’kukonzekera mmene tingawayankhire. (Akol. 4:6) Mwachitsanzo ena angafune kudziwa kuti: ‘Kodi kumwamboko kukachitika zotani?’ ‘Ukatenga nthawi yaitali bwanji?’ ‘Kodi ndiyenera kuvala chiyani?’ ‘Kodi pafunika ndalama yoti ndikalipire?’ ‘Kodi kukakhala kuyendetsa mbale ya zopereka?’ Tikamaitanira munthu ku Chikumbutso, tingamufunse kuti, “Kodi muli ndi funso lililonse?” kenako n’kuyankha mafunso omwe angakhale nawo. Tingagwiritsenso ntchito mavidiyo akuti Tizikumbukira Imfa ya Yesu komanso Kodi pa Nyumba ya Ufumu Pamachitika Zotani? pofuna kuthandiza munthu kudziwa mmene misonkhano yathu imachitikira. Komanso mu phunziro 28 mu buku la Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale, muli mfundo zambiri zabwino zomwe tingakambirane naye.

16. Kodi anthu amene apezeka pa Chikumbutso angakhale ndi mafunso ati?

16 Pambuyo pa Chikumbutso, anthu achidwi omwe anabwera angakhale ndi mafunso. Iwo angadabwe kuti ndi anthu ochepa chabe (ngati analipo) omwe anadya zizindikiro. Angafunenso kudziwa kuti timachita mwambo wa Chikumbutsowu kangati. Komanso angafune kudziwa ngati misonkhano ya Mboni za Yehova imachitika m’njira yofananayo. Ngakhale kuti zambiri mwa mfundozi zimafotokozedwa mu nkhani ya pa Chikumbutso, anthu atsopanowa amafunika kuwafotokozera mwatsatanetsatane. Nkhani ya pa jw.org yakuti “N’chifukwa Chiyani a Mboni za Yehova Mumachita Mwambo wa Mgonero wa Ambuye Mosiyana ndi Zipembedzo Zina?” ingatithandize kuwayankha mafunso omwe angakhale nawo. Tikufuna kuchita zomwe tingathe kuti tithandize anthu a “maganizo abwino” kupindula ndi mwambowu Chikumbutso chisanachitike, chikamadzachitika komanso pambuyo pake.​—Mac. 13:48.

MUDZATHANDIZE AMENE ANASIYA KUSONKHANA

17. Kodi akulu angathandize bwanji anthu amene anasiya kusonkhana? (Ezekieli 34:12, 16)

17 Pa nyengo ya Chikumbutso, kodi akulu angathandize bwanji anthu amene anasiya kusonkhana? Mudzawasonyeze kuti mumawaganizira. (Werengani Ezekieli 34:12, 16.) Chikumbutso chisanachitike, mudzayesetse kulankhula ndi abale ndi alongo amenewa. Atsimikizireni kuti mumawakonda komanso kuti mukufunitsitsa kuwathandiza mmene mungathere. Aitanireni ku Chikumbutso. Akadzabwera mudzawalandire ndi manja awiri. Pambuyo pa Chikumbutso, muzidzalankhulabe ndi abale ndi alongo okondedwawa ndipo muzichita chilichonse chomwe mungathe kuti muwathandize kubwerera kwa Yehova.​—1 Pet. 2:25.

18. Kodi tonsefe tingathandize bwanji anthu amene anasiya kusonkhana? (Aroma 12:10)

18 Kodi anthu onse mumpingo angathandize bwanji anthu amene anasiya kusonkhana, omwe apezeka pa Chikumbutso? Angatero pochita nawo zinthu mwachikondi, mokoma mtima komanso mwaulemu (Werengani Aroma 12:10.) Dziwani kuti abale ndi alongowo, omwe ndi nkhosa za mtengo wapatali, ayenera kuti ankakayikira zoyambiranso kubwera kumisonkhano. Mwina ankaopa kuti sadzalandiridwa bwino.e Choncho muzipewa kuwafunsa mafunso omwe angawachititse manyazi kapena kulankhula zinthu zomwe zingawapweteke. (1 Ates. 5:11) Abale ndi alongowa ndi Akhristu anzathu ndipo tikusangalala kuti tayambiranso kusonkhana nawo.​—Sal. 119:176; Mac. 20:35.

Zithunzi: 1. M’bale yemwe anasiya kusonkhana wanyamula buku la nyimbo ndi Baibulo ndipo akuchita manyazi kuti akalowe m’Nyumba ya Ufumu. Waima chapatali n’kumaona abale ndi alongo akufika ku Chikumbutso. 2. Pambuyo pake iye akusangalala kucheza ndi m’bale wina m’Nyumba ya Ufumu.

Kodi Abale ndi Alongo Anachita Zotani?

“Ndinkachita manyazi kupita ku Nyumba ya Ufumu. Sindinkadziwa mmene abale ndi alongo angakandilandirire. Mlongo wina wachikulire yemwe tinkasonkhana naye zaka 30 zapitazo anandiuza kuti, ‘Walandiridwa mwana wanga.’ Ndinasangalala ndipo zinandilimbikitsa. Tsopano ndinali womasuka.”​—JAVIER.

“Ndinapita ku Nyumba ya Ufumu ndipo ndinakhala mpando wakumbuyo n’cholinga choti anthu ena asandione. Komabe ambiri anazindikira kuti ndinkabwera kumisonkhanoko ndili mwana. Anandilandira komanso kundihaga moti ndinamva bwino mumtima. Zinali ngati ndafika kunyumba.”​—MARCO.

19. Kodi kukumbukira imfa ya Yesu kumatithandiza bwanji?

19 Timayamikira kuti Yesu anakonza zoti chaka ndi chaka tizichita mwambo wokumbukira imfa yake. Mwambowu umatithandiza ifeyo komanso anthu ena m’njira zambiri. (Yes. 48:17, 18) Timayamba kukonda kwambiri Yehova ndi Yesu. Timasonyeza kuti timayamikira kwambiri zimene atichitira. Timayamba kugwirizana kwambiri ndi Akhristu anzathu. Komanso tingathandize ena kudziwa kuti angathe kudzasangalala ndi madalitso amene amatheka chifukwa cha dipo. Tiyeni tichite zonse zomwe tingathe kuti tikonzekere kudzapezeka pa tsiku la Chikumbutso, lomwe ndi lofunika kwambiri pa chaka.

M’chaka chino cha 2024, Chikumbutso chidzachitika Lamlungu. Zikatere sipakhala misonkhano ya kumapeto kwa mlungu. Pachifukwa chimenechi, palibe nkhani yophunzira mlungu wamawa.

KODI TINGATANI KUTI . . .

  • tikonzekeretse mtima wathu pa nthawi ya Chikumbutso?

  • tithandize ena kudzapindula ndi mwambowu?

  • tithandize amene anasiya kusonkhana?

NYIMBO NA. 18 Tikuthokoza Chifukwa cha Dipo

a Mungagwiritse ntchito malo ofufuzira pa jw.org kuti mupeze nkhani ndi mavidiyo omwe atchulidwa munkhaniyi.

b Onani nkhani yakuti “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” mu Nsanja ya Olonda ya April 2021.

c Onani buku lakuti Yandikirani kwa Yehova, mutu 23, ndime 8-9.

d Onani bokosi lakuti “Zothandiza Pofufuza.”

e Onani zithunzi komanso bokosi lakuti “Kodi Abale ndi Alongo Anachita Zotani?” M’bale yemwe anasiya kusonkhana akuchita manyazi kuti akalowe mu Nyumba ya Ufumu, koma kenako akulimba mtima n’kukalowa. Akulandiridwa bwino ndipo akucheza ndi Akhristu anzake.

f MAWU OFOTOKOZERA ZINTHUNZI: Pamene anthu a Yehova akuchita Chikumbutso kumbali ina ya dzikoli, abale ndi alongo kumbali ina akukonzekera kuchita mwambowu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena