NYIMBO 18
Tikuthokoza Chifukwa cha Dipo
Losindikizidwa
1. Tsopano tabwera
Kwa inu Yehova
Chifukwa munatisonyezadi
Chikondi.
Munapereka Mwana
Wanu woyamba
Monga nsembe yoposa ina
Iliyonse.
(KOLASI)
Anafera anthu tonse
Kuti tidzapulumuke.
Tikuthokoza ndi mtima wonse
Inu M’lungu.
2. Mofunitsitsa Yesu
Anapereka
Nsembe ya dipo ndipo
Tikusangalala.
Asanabwere
Kudzapereka dipo,
Sitinkayembekezera
Moyo wosatha.
(KOLASI)
Anafera anthu tonse
Kuti tidzapulumuke.
Tikuthokoza ndi mtima wonse
Inu M’lungu.
(Onaninso Aheb. 9:13, 14; 1 Pet. 1:18, 19.)