Salimo
Kwa wotsogolera nyimbo. Aimbe nyimboyi pa Yedutuni.* Nyimbo ndi Salimo la Asafu.+
2 Pa tsiku limene ndakumana ndi mavuto ndimafunafuna Yehova.+
Usiku ndimakweza manja anga kwa iye ndipo sindisiya.*
Palibe chimene chimanditonthoza.
3 Ndikakumbukira Mulungu ndimabuula.+
Ndimavutika kwambiri mumtima ndipo mphamvu zanga zimatha.*+ (Selah)
4 Mumatsegula zikope zanga.
Ndavutika mumtima, moti sindingathe kulankhula.
7 Kodi Yehova adzatitaya mpaka kalekale?+
Kodi sadzatisonyezanso kukoma mtima kwake?+
8 Kodi chikondi chake chokhulupirika chatha mpaka kalekale?
Kodi malonjezo ake sadzakwaniritsidwa ku mibadwomibadwo?
9 Kodi Mulungu waiwala kusonyeza kukoma mtima kwake,+
Kapena kodi mkwiyo wake wachititsa kuti chifundo chake chithe? (Selah)
10 Kodi ndizingonena kuti: “Zimene zikundivutitsa* ndi zakuti:+
Wamʼmwambamwamba wasiya kutithandiza”?
11 Ndidzakumbukira ntchito za Ya,
Ndidzakumbukira zochita zanu zodabwitsa zakale.
13 Inu Mulungu, njira zanu ndi zoyera.
Kodi pali mulungu winanso wamkulu amene angafanane ndi inu Mulungu?+
14 Inu ndinu Mulungu woona amene mumachita zinthu zodabwitsa.+
Mwasonyeza ku mitundu ya anthu kuti ndinu wamphamvu.+
Ndipo madzi akuya anayamba kuvutika kwambiri.
17 Mitambo inagwetsa madzi.
Mʼmitambo yakuda munamveka mabingu,
Ndipo mphezi zanu zinawala paliponse ngati mivi.+
18 Phokoso la bingu lanu+ linali ngati la mawilo a galeta.
Kungʼanima kwa mphezi kunaunika padziko lapansi.+
Dziko lapansi linanjenjemera komanso kugwedezeka.+