Ndandanda ya Mlungu wa March 8
MLUNGU WOYAMBIRA MARCH 8
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
lv mutu 4 ndime 12-21 ndi bokosi la patsamba 42a
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 1 Samueli 1-4
Na. 1: 1 Samueli 2:18-29
Na. 2: Kodi Yesu Anaphunzitsa Kuti Oipa Amazunzidwa Akamwalira? (rs tsa.149 ndime 6)
Na. 3: Malemba Amasonyeza Kuti Yehova Amakonda Ana
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 10: Kodi Mukamalalikira Uthenga wa m’Baibulo Mumalankhula Momveka? Nkhani yochokera mu buku la Sukulu ya Utumiki, kuyambira patsamba 109, ndime 2 mpaka kumapeto kwa mutuwo.
Mph. 20: “Zimene Tingachite Poyamikira Mphatso Yaikulu Kwambiri Imene Mulungu Anatipatsa.” Kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Mukatha kukambirana ndime 3, fotokozaninso zimene mpingowo wakonza pantchito yapadera yogawira timapepala toitanira anthu ku Chikumbutso. Pemphani mpainiya wothandiza kuti achite chitsanzo cha mmene angagawirire kapepala koitanira anthu ku Chikumbutso. Akatha, m’funseni kuti anene zimene anachita kuti apeze nthawi yochita upainiya wothandiza komanso anene mmene wapindulira.
[Mawu a M’munsi]
a Mungasankhe kukambirana bokosi kapena ayi.