Nyimbo 8
Mgonero wa Ambuye
Losindikizidwa
1. Atate wathu wakumwamba,
Usikuwu n’ngwapadera!
Pa Nisani fotini panaoneka
Chikondi, nzeru ndi mphamvu.
Mwanawankhosa anadyedwa,
Is’raeli namasuka.
Kenako Mbuye anakhetsa magazi
Kukwaniritsa ulosiwo.
2. Tasonkhana pamaso panu.
Tadza ngati nkhosa zanu
Kukutamandani pa chikondi chanu,
Dzina lanu tilikweze.
Tisunge Chikumbutso ichi,
m’mitima ndi m’maganizo.
Tidzamutsatira Khristu nthawi zonse
Kuti tidzaupeze moyo.
(Onanino Luka 22:14-20; 1 Akor. 11:23-26.)