Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 2/10 tsamba 8
  • Zomwe Munganene Pogawira Magazini

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zomwe Munganene Pogawira Magazini
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2010
  • Nkhani Yofanana
  • Zomwe Munganene Pogawira Magazini
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
  • Zomwe Munganene Pogawira Magazini
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
  • Zomwe Munganene Pogawira Magazini
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2010
  • Zomwe Munganene Pogawira Magazini
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2010
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2010
km 2/10 tsamba 8

Zomwe Munganene Pogawira Magazini

Nsanja ya Olonda February 1

“Ambirife tili ndi chipembedzo chathu. Koma kodi mukuganiza kuti Mulungu zimam’khudza tikasankha kumulambira mwa njira inayake? [Yembekezani ayankhe. Kenako werengani Mateyo 15:9.] Munkhani ino muli mfundo zinayi zimene Yesu anafotokoza zomwe zingakuthandizeni kudziwa chipembedzo choona.” M’sonyezeni nkhani imene yayambira patsamba 16.

Galamukani! February

“Ena amakhulupirira kuti kuli Mlengi, pomwe ena amatsutsa n’kumanena kuti zimenezo n’zosagwirizana ndi sayansi ndiponso n’zosamveka. Kodi inuyo mukuganiza bwanji? [Yembekezani ayankhe.] Mogwirizana ndi Baibulo, kuti munthu akhale ndi chikhulupiriro chenicheni, ayenera kukhala ndi umboni wa zomwe akukhulupirirazo. [Werengani Aheberi 11:1.] Nkhani iyi ikufotokoza umboni wosonyeza kuti kuli Mlengi.” M’sonyezeni nkhani imene yayambira patsamba 22.

Nsanja ya Olonda March 1

“Kodi inuyo mumaganiza kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu, kapena langokhala buku labwino basi? [Yembekezani ayankhe.] Taonani zimene Baibulo likunena. [Werengani 2 Timoteyo 3:16, 17.] Magazini iyi ili ndi mfundo zimene zingakuthandizeni kudziwa zoona pankhaniyi ndiponso chifukwa chake kudziwa zimenezo kuli kofunika.”

Galamukani! March

“Mofanana ndi anthu ambiri, inunso muyenera kuti mumachita chidwi ndi zinthu zachilengedwe. Kodi mumadziwa kuti zinthu zimenezi zimasonyeza kuti pali winawake wanzeru amene anazilenga? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno werengani Salmo 104:24.] Magazini ino ikufotokoza zina mwa zinthu zachilengedwe zimene zinapangidwa mwaluso kwambiri ndiponso zimene ifeyo tikuphunzirapo.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena