Ndandanda ya Mlungu wa March 15
MLUNGU WOYAMBIRA MARCH 15
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
lv mutu 4, ndi mabokosi a pamasamba 46-49
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 1 Samueli 5-9
Na. 1: 1 Samueli 6:1-9
Na. 2: Kodi Tingadziteteze Bwanji kwa Satana ndi Ziwanda Zake?
Na. 3: Kodi Fanizo la Munthu Wachuma ndi Lazaro Limatanthauza Chiyani? (rs tsa.150 ndime 1 mpaka tsa.151 ndime 1)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 15: “Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira.” Kambiranani ndi omvera. Pemphani omvera kuti atchule mbali zolimbikitsa za lipoti la pachaka limene lili mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa February 2010.
Mph. 15: “Ntchito Yofunika Kwambiri Kuposa Zonse.” Kukambirana mwa mafunso ndi mayankho. Mukatha kukambirana ndime 3, funsani wofalitsa amene anachititsapo phunziro la Baibulo lopita patsogolo. Kodi wophunzira Baibuloyo anafunika kusintha zotani pamoyo wake? Kodi zimenezi zimamukhudza bwanji wofalitsayo?