Chikumbutso
Kodi Mudzachita Zinthu Zosonyeza Kuyamikira Yehova pa Nyengo ya Chikumbutso Ikubwerayi?
1. Kodi pa nthawi ya Chikumbutso tidzakhala ndi mwayi wotani?
1 Pa nthawi ya Chikumbutso, chomwe chidzachitike pa April 14, tidzakhala ndi mwayi wosonyeza kuyamikira zinthu zabwino zomwe Yehova anatichitira. Nkhani yopezeka pa Luka 17:11-18, imasonyeza kuti Yehova ndi Yesu amakondwera ndi anthu amene amasonyeza mtima woyamikira. N’zomvetsa chisoni kuti pa anthu akhate 10 amene Yesu anawachiritsa, ndi mmodzi yekha amene anapitanso kwa Yesu kukathokoza. Mphatso ya dipo la Yesu idzapangitsa kuti anthu asamadzadwalenso koma azidzakhala ndi moyo wosatha. N’zosakayikitsa kuti nthawi zonse tizidzayamikira Yehova chifukwa cha madalitso amenewa. Koma kodi milungu ikubwerayi tidzasonyeza bwanji kuti timayamikira Yehova pa zimene anatichitira?
2. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira dipo?
2 Khalani ndi Mtima Woyamikira: Kuyamikira kumayambira mumtima. Choncho pofuna kutithandiza kuti tikhale ndi mtima woyamikira, tapatsidwa ndandanda ya kuwerenga Baibulo imene ikupezeka m’mabuku osiyanasiyana monga mu Kalendala komanso m’kabuku ka Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku. Mungachite bwino kumadzawerengera limodzi mavesi amenewa ndi banja lanu. Zimenezi zingathandizenso kuti tizikhala ndi makhalidwe abwino.—2 Akor. 5:14, 15; 1 Yoh. 4:11.
3. Tchulani njira zimene tingadzasonyezere kuyamikira pa nyengo ya Chikumbutso?
3 Sonyezani Kuti Ndinu Woyamikira: Munthu amasonyeza kuyamikira ndi zochita zake. (Akol. 3:15) Munthu wakhate uja, chifukwa choti anali ndi mtima woyamikira, anayesetsa kufunafuna Yesu kuti amuthokoze. N’zosakayikitsa kuti ankauzanso anthu ena mosangalala kuti wachiritsidwa. (Luka 6:45) Kodi nafenso tingadzagwire nawo mwakhama ntchito yoitanira anthu ku Chikumbutso posonyeza kuyamikira dipo? Kuchita upainiya wothandiza kapena kuwonjezera zochita mu utumiki ndi njira inanso imene tingadzasonyezere kuti timayamikira dipo. Madzulo a tsiku la Chikumbutsolo, tingadzasonyezenso mtima woyamikira polandira alendo amene adzabwere komanso kuyankha mafunso amene angadzakhale nawo.
4. Kodi mungatani kuti nyengo ya Chikumbutso ikapita musadzaidandaule?
4 Kodi Chikumbutsochi chidzakhala chomaliza? (1 Akor. 11:26) Sitikudziwa. Koma zimene tikudziwa ndi zoti Chikumbutso cha chaka chino chikapita, chapita, choncho ndi bwino kugwiritsa ntchito nthawi ya Chikumbutsoyi kusonyeza kuyamikira kwathu. Kodi inuyo mudzachita zimenezi? Tiyeni tiyesetse kuti zolankhula komanso zoganiza zathu zizisangalatsa Yehova yemwe anapereka mowolowa manja nsembe ya dipo.—Sal. 19:14.