Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 2/08 tsamba 1
  • Kumbukirani Dipo ndi Mtima Woyamikira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kumbukirani Dipo ndi Mtima Woyamikira
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
  • Nkhani Yofanana
  • “Muzichita Zimenezi” Chikumbutso Chidzachitika pa April 5
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2012
  • Tiyeni Tisonyeze Kuyamikira
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
  • “Muzichita Zimenezi Pondikumbukira Ine”
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
  • Kugawira Timapepala Toitanira Anthu ku Chikumbutso
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2010
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
km 2/08 tsamba 1

Kumbukirani Dipo ndi Mtima Woyamikira

1, 2. Kodi tili ndi zifukwa zotani zokumbukira dipo ndi mtima woyamikira?

1 Pomvera lamulo la Yesu, Akhristu padziko lonse adzakumana Loweruka pa March 22, 2008 kuti akumbukire imfa ya Yesu Khristu. (Luka 22:19; 1 Akor. 11:23-26) Timasangalala kuchita zimenezi chifukwa choyamikira zimene zinachitika pa tsiku limeneli zaka 1,975 zapitazo. Popitirizabe kukhala munthu wolungama panthawi imene amafa imfa yopweteka pa mtengo wozunzikirapo, Yesu anayeretsa dzina la Atate ake. Mwa kuchita zimenezi, Yesu anapereka yankho labwino kwambiri ku mawu otonza a Satana.—Yobu 1:11; Miy. 27:11.

2 Magazi amene Yesu anakhetsa analimbikitsa pangano latsopano, n’kuchititsa kuti anthu opanda ungwiro atengedwe kukhala ana a Mulungu n’kukhala ndi chiyembekezo chodzalamulira ndi Khristu mu Ufumu wa kumwamba. (Yer. 31:31-34; Maliko 14:24) Komanso, kukula kwa chikondi cha Mulungu kunaonekera bwino atapereka nsembe Mwana wake wokondedwa, monga mmene Yesu mwiniwake anauzira Nikodemo.—Yoh. 3:16.

3. Kodi anthu amene adzabwere ku Chikumbutso adzapindula bwanji?

3 Itanani Ena: Utumiki Wathu wa Ufumu wa January unati tiyenera kulemba mayina a anthu owadziwa ndi kuwaitana aliyense payekha. Kodi mwayamba kale kuitana anthu amene munawalemba mayina? Kodi mukukonzekera kuchita ntchito yapadera yoitanira anthu ku Chikumbutso yomwe iyambe pa March 1? Amene adzabwere adzamva nkhani ya m’Malemba imene idzawalimbikitsa kukhala ndi chikhulupiriro mwa dipo, chimenenso chimatsogolera ku moyo wosatha.—Aroma 10:17.

4. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kudzafika msanga ku Chikumbutso?

4 Onse amene adzakwanitse kubwera ayenera kukonza zodzafika msanga kuti adzalandire anthu amene anawaitana. Popeza kuti ku Chikumbutso kumabwera anthu ambiri, ndi bwino kuti tidzaonetsetse kuti tidziwe anthu atsopano ndi amene amabwera ku misonkhano yathu mwa apo ndi apo.

5. Kodi mungakonzekeretse bwanji mtima wanu podzachita mwambo umenewu?

5 Konzekeretsani Mtima Wanu: Kabuku ka Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku ka 2008 ndi kalendala ya 2008, zili ndi ndandanda ya kuwerenga Baibulo kwa pa Chikumbutso kuyambira pa March 17. Kuganizira zinthu zofunika kwambiri zimene zinachitika kumapeto kwa moyo wa Yesu padziko lapansi, kudzakuthandizani kukonzekeretsa mtima wanu kuchita mwambo wa Chikumbutso. (Ezara 7:10) Kupemphera ndiponso kusinkhasinkha nkhani za m’Baibulo zimenezi, kudzakuthandizani kuyamikira kwambiri chikondi chimene Yehova ndi Mwana wake anasonyeza popereka dipo.—Sal. 143:5.

6. Kodi ubwino woyamikira kwambiri dipo ndi wotani?

6 Pamene nyengo ya Chikumbutso ikuyandikira, tiyeni tikonzekere bwino ndi kukonzekeretsa ena kaamba ka mwambo wofunika kwambiri umenewu. Kukumbukira dipo ndi mtima woyamikira kudzalimbikitsa ubale wathu ndi Yehova komanso Mwana wake. (2 Akor. 5:14, 15) Kudzatilimbikitsanso kuwatsanzira posonyeza ena chikondi chopanda dyera.—1 Yoh. 4:11.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena