Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu Woyambira March 13
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zina musankhe mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno. Gwiritsani ntchito mfundo zimene zili patsamba 4 kapena ulaliki wina uliwonse umene ungakhale wothandiza m’gawo lanu kuchitira chitsanzo chosonyeza mmene tingagawire Nsanja ya Olonda ya March 15 ndi Galamukani! ya March. Kumapeto kwa chitsanzo chilichonse, wofalitsa agwiritse ntchito tsamba lomaliza la magazini imene akugawira kuitanira mwininyumba ku Chikumbutso. (Ngati mpingo wanu sunalandire magazini tatchulawa gwiritsirani ntchito zitsanzo zimene zinatchulidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi wathawo.)
Mph. 15: “Thandizani Ena Kupindula ndi Dipo.”a Nkhani imene ikambidwe ino ikatha ifotokoza mfundo zina zowonjezera za mmene tingagwiritsire ntchito masamba 206 mpaka 209 a buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani poitanira anthu ku Chikumbutso.
Mph. 20: Mgonero wa Ambuye Ndi Mwambo Umene Umalemekeza Mulungu. Kukambirana mwa mafunso ndi mayankho kuchokera m’buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani, masamba 206 mpaka 209. M’mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, sonyezani mmene mungayambire kukambirana nkhaniyi ndi mwininyumba mwa kuwerenga ndime yoyamba. Popanda kuwerenga ndime, pemphani omvera kupereka ndemanga pa mafunso otsatirawa: (ndime 2) Kodi Yesu anayambitsa liti mwambo wa Chikumbutso cha imfa yake? (ndime 3) Kodi Mgonero wa Ambuye uyenera kuchitika kangati pachaka? (ndime 4) Kodi Baibulo limaufotokoza bwanji mwambo wa Chikumbutso? (ndime 5) Kodi timadziwa bwanji kuti Yesu sanasandutse mkate kukhala thupi lake lenileni ndiponso vinyo kukhala mwazi wake? (ndime 6) Kodi mkate wopanda chotupitsa umaimira chiyani? (ndime 7) Kodi vinyo wofiira amaimira chiyani? (ndime 8) Kodi ndani okha amene ayenera kudya mkate ndi kumwa vinyo? (ndime 9) Kodi Chikumbutso chimachitika liti chaka chilichonse, ndipo n’chifukwa chiyani tiyenera kupezekapo? Kambiranani malemba ofunika ngati nthawi ilola. Limbikitsani onse kuphunzira nkhaniyi ndi omwe amaphunzira nawo Baibulo ndiponso ena amene amawaitanira ku Chikumbutso. Pophunzira werengani ndime, kambiranani mfundo zazikulu, ndipo gwiritsani ntchito mafunso osavuta monga omwe ali mu nkhani ino.
Nyimbo Na. 134 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira March 20
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Kambani mfundo zazikulu za m’bokosi lakuti “Zofunika Kukumbukira pa Chikumbutso.” Tchulaninso madeti ndi malo a msonkhano wanu wachigawo wa 2006 wakuti “Chipulumutso Chayandikira.”
Mph. 23: Udindo wa Kristu pa Makonzedwe a Mulungu. Nkhani yochokera m’buku lakuti Gulu Lochita Chifuniro cha Yehova, masamba 10 mpaka 13. Pofotokoza ndime ziwiri zoyambirira pansi pa kamutu kakuti “Udindo Umene Kristu Ali Nawo,” gwiritsani ntchito mphindi zitatu kapena zinayi kufotokoza ndi kuchitira chitsanzo njira zogwiritsira ntchito timapepala toitanira anthu ku Chikumbutso. Tchulani mwachidule mfundo zimene zili mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa February 2006, tsamba 3 ndime 3.
Mph. 12: Kulimbikitsidwa mwa Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku. Nkhani ndi chitsanzo kuchokera pa mawu oyamba a m’kabuku ka Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku—2006. Konzani chitsanzo chosonyeza banja likuphunzira lemba la tsiku la lero ndi ndemanga zake.
Nyimbo Na. 103 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira March 27
Mph. 15: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kupereka maola a utumiki wa kumunda a mwezi wa March. Werengani lipoti la maakaunti ndi mawu oyamikira zopereka amene alembedwa pa sitetimenti. Gwiritsani ntchito mfundo zimene zili patsamba 4 kapena ulaliki wina uliwonse umene ungakhale wothandiza m’gawo lanu kuchitira zitsanzo zosonyeza mmene tingagawire Nsanja ya Olonda ya April 1 ndi Galamukani! ya April. Sonyezaninso momwe tingagwiritsire ntchito kapepala koitanira anthu achidwi ku Chikumbutso. (Ngati mpingo wanu sunalandire magazini tatchulawa gwiritsirani ntchito zitsanzo zimene zinatchulidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi wathawo.)
Mph. 10: Ndani Amene Ali Woyenera Kulamulira Dziko? Nkhani ndi chitsanzo kuchokera pa tsamba lomaliza la Nsanja ya Olonda ya April 1, 2006. Gwiritsani ntchito mpata uliwonse umene mwapeza kuitanira anthu ku nkhani ya onse yapadera imeneyi. Yesetsani kuitana wophunzira Baibulo aliyense komanso azibale ake amene mwina sakhala nawo pa phunziro la Baibulolo. Anthu achidwi onse amene tikuwadziwa komanso anthu ena amene timakumana nawo mu utumiki wa kumunda tiyenera kuwaitanira ku nkhani yapaderayi. Khalani ndi chitsanzo chosonyeza momwe tingagwiritsire ntchito Nsanja ya Olonda ya April 1 poitana munthu amene wasiya kulalikira kapena amene wasiya kubwera ku misonkhano.
Mph. 20: Zokumana nazo za pampingo. Pemphani omvera kuti afotokoze zimene anakumana nazo pogawira buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani m’mwezi wa March. Tchulani za maphunziro a Baibulo amene anthu anayambitsa. Mungachite chitsanzo chimodzi kapena ziwiri zosonyeza zokumana nazo zabwino kwambiri.
Nyimbo Na. 170 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira April 3
Mph. 15: Zilengezo za pampingo. Tchulani mwachidule mfundo zomwe zili mu nkhani yakuti “Sangalalani Pophunzira Buku Lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?” yomwe ili pa tsamba 6 la Utumiki Wathu wa Ufumu wa February 2006. Tchulani za ndandanda yophunzirira buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. Sonyezaninso mmene tingagwiritsire ntchito timapepala toitanira anthu achidwi ku Chikumbutso.
Mph. 10: Zosowa za pampingo.
Mph. 20: Kodi Armagedo N’chiyani? Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho pogwiritsa ntchito masamba 37 mpaka 42 a mu buku la Kukambitsirana. Pemphani omvera kuti apereke ndemanga pa mafunso amene ali ndi zilembo zakuda kwambiri, pogwiritsa ntchito malemba ogwidwa mawu ndi amene angotchulidwa. Kambiranani mmene tingagwiritsire ntchito mfundo zimenezi mu utumiki wa kumunda.
Nyimbo Na. 93 ndi pemphero lomaliza.
[Mawu a M’munsi]
a Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.