Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda Feb. 15
“Ngati mukadapatsidwa mwayi wosankha munthu woti alamulire dziko, kodi mukadasankha ndani? [Yembekezani ayankhe.] Nsanja ya Olonda iyi ikufotokoza chifukwa chake Mulungu wasankha Mesiya kuti alamulire dziko. Ikufotokozanso zinthu zimene Mesiyayo adzachitira dziko lapansi akadzayamba kulamulira.” Werengani Yesaya 9:6, 7.
Galamukani! Feb.
“Masiku ano kuli milungu yambiri imene anthu amailambira. Komabe, taonani zimene Yesu ananena m’pemphero zokhudza Atate ake akumwamba. [Werengani Yohane 17:3.] Ngati kuli Mulungu mmodzi yekha woona, bwanji nanga za milungu ina? [Yembekezani ayankhe.] Nkhani iyi ikufotokoza za zimene Baibulo limanena.” Aonetseni nkhani ya pamasamba 28 ndi 29.
Nsanja ya Olonda Mar. 1
“Anthu ambiri amavomereza kuti tizikondana wina ndi mnzake, monga mmene Yesu analamulira pa lemba ili. [Werengani Yohane 13:34, 35.] Komano, kodi tingawapeze anthu amene amagwiritsadi ntchito chiphunzitso cha Yesu chimenechi pa moyo wawo? [Yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikufotokoza mmene tingadziwire Akristu oona masiku ano.”
Galamukani! Mar.
“Chikondi n’chofunika kuti tikhale ndi moyo wabwino ndi wosangalala. Komabe, anthu ambiri masiku ano alibe chikondi. Kodi n’chifukwa chiyani zinthu zili choncho. [Yembekezani ayankhe.] Chinthu chimodzi chimene chingathandize kuti anthu azitikonda ndicho kuwakonda mopanda dyera. Magazini iyi ikufotokoza mmene mungachitire zimenezo.” Werengani 1 Akorinto 13:4-7.