Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini
Nsanja ya Olonda Feb. 15
“Anthu ena amadabwa ngati kunja kuno kuli Mulungu amene ali ndi umunthu wakewake. Ena amati alipo koma amaganiza kuti ali kutali ndi iwowo. Kodi inunso mumaganiza choncho? [Yembekezani ayankhe.] Taonani chifukwa chake kudziŵa Mulungu ndi umunthu wake kuli kofunika kwambiri. [Ŵerengani Yohane 17:3.] Mudzasangalala kwambiri kuŵerenga nkhani zoyambirira m’magazini iyi.”
Galamukani! Feb. 8
“Ndili ndi funso limene ndikufunsa aliyense m’dera lino. Kodi pali tchimo limene Mulungu sakhululukira? [Yembekezani ayankhe.] Baibulo limati lilipo tchimo lina limene Mulungu sakhululukira. Taŵerengani apa. [Ŵerengani Mateyu 12:31.] M’magazini iyi muli nkhani imene ikufotokoza mawu amene tangoŵerenga kumeneŵa.”
Nsanja ya Olonda Mar. 1
“Ndikufuna mundiuze maganizo anu pa lemba lofunika kwambiri ili. [Ŵerengani Mateyu 5:10.] Kodi munthu angakhale bwanji wosangalala pamene akuzunzidwa? [Yembekezani ayankhe.] Nkhani ziŵiri zoyambirira m’magazini iyi zikufotokoza mmene ena anakhalirabe osangalala ngakhale kuti amazunzika. Ndikhulupirira kuti mudzasangalala kuŵerenga za mmene anachitira zimenezo.”
Galamukani! Feb. 8
“Galamukani! iyi ikusimba zinthu zomvetsa chisoni zimene zikuchitika masiku ano zokhudza uhule wa ana. Baibulo likulonjeza kuti nkhanza ya ana yonyansa ngati imeneyi itha posachedwa. [Ŵerengani Miyambo 2:21, 22.] Magazini iyi ikusonyeza chimene chikuchititsa kuzunza ana mwanjira imeneyi komanso mmene vutoli lithere.”