Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini
Nsanja ya Olonda Feb. 15
“Anthu ambiri amavutika maganizo chifukwa cha zoipa zimene zachitidwa m’dzina la chipembedzo. Ambiri akuganiza kuti chipembedzo n’chimene chikuchititsa mavuto a anthu. Kodi munaganizapo zimenezi? [Yembekezani ayankhe. Kenako ŵerengani Chivumbulutso 18:24.] Magazini iyi ikufotokoza zimene Baibulo limanena pankhani imeneyi.”
Galamukani! Feb. 8
“Dzina lenileni la Mulungu limaoneka chonchi m’chinenero cha Chihebri. [M’sonyezeni pachikuto.] Anthu ena amakhulupirira kuti dzinali lisamatchulidwe. Ena amalitchulatchula. Galamukani! iyi ikufotokoza za nkhani imeneyi. Ikufotokozanso mmene tingadziŵire dzina la Mulungu.” Ŵerengani Salmo 83:18.
Nsanja ya Olonda Mar. 1
“Nthaŵi ina, Yesu Kristu anafunsidwa kuti: ‘Lamulo la m’tsogolo la onse ndi liti?’ Onani yankho lake. [Ŵerengani Marko 12:29, 30.] Kodi munadzifunsapo kuti Yesu anali kutanthauza chiyani? [Yembekezani ayankhe.] Nkhani yakuti ‘Mmene Timasonyezera Kuti Timakonda Mulungu’ ikufotokoza tanthauzo la mawu odziŵika kwambiri ameneŵa.”
Galamukani! Feb. 8
“Anthu ambiri masiku ano amagwira ntchito kwambiri ndipo amafunika kupuma mokwanira. Mwina mungavomereze mawu aŵa amene analembedwa zaka zoposa 3,000 zapitazo. [Ŵerengani Mlaliki 4:6. Ndiyeno m’loleni akambepo.] Galamukani! iyi ili ndi mfundo zothandiza za momwe tingadziŵire kuti tili ndi vuto la kusagona mokwanira ndiponso mmene tingathetsere vutolo.”