Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda Feb. 15
“Anthu ena amaona kuti anthu ndiye akuwononga dziko. Kodi zimenezo zinayamba zakudetsanipo nkhawa? [Yembekezani ayankhe.] Taonani lonjezo lolimbikitsa ili. [Werengani Chivumbulutso 11:18] Magaziniyi ili ndi nkhani imene ikusonyeza chimene chimapangitsa dziko lapansili kukhala lapadera poliyekezera ndi mayiko ena. Ikusonyezanso zimene Baibulo limanena zokhudza tsogolo la dziko lapansi.”
Galamukani! Feb.
“Kodi mukuganiza kuti izi n’zimene zachititsa mavuto ochuluka padziko pano? [Werengani 1 Yohane 5:19. Kenako yembekezerani ayankhe] Nkhaniyi ikusonyeza zimene Baibulo limanena za ‘woipayo’ ndiponso mmene tingapewere kuti asatisocheretse.” Asonyezeni nkhani imene yayambira pa tsamba 12.
Nsanja ya Olonda Mar. 1
“Anthu ambiri amaganiza kuti zipembedzo zonse n’zovomerezeka kwa Mulungu. Kodi mukuganiza kuti palibe vuto lililonse ngati munthu atasankha chipembedzo chilichonse chimene wakonda? [Yembekezani ayankhe.] Taonani mfundo iyi. [Werengani 1 Yohane 4:1.] Magaziniyi ikufotokoza mmene tingayesere zimene chipembedzo chimaphunzitsa kuti tione ngati zikuchokera kwa Mulungu. Ikufotokozanso mmene zipembedzo zosiyanasiyana zinayambira.”
Galamukani! Mar.
“Kodi mukuganiza kuti ena mwa mavuto amene achinyamata amakumana nawo masiku ano ndi ati? [Yembekezani ayankhe] Lemba ili likunena za vuto limodzi, vuto lopeza anzawo abwino. [Werengani Miyambo 13:20.] Magaziniyi ikufotokoza kuopsa kogwiritsa ntchito Intaneti popeza anzawo ndiponso mmene achinyamata angatetezedwere ku vuto limeneli.”