Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda Feb. 1
“Kodi mukuganiza kuti zinthu zingayende bwanji m’banja ngati mwamuna ndi mkazi wake atagwiritsa ntchito malangizo awa? [Werengani Aefeso 4:31. Ndiyeno yembekezani ayankhe.] Nkhani iyi ikufotokoza mfundo za m’Baibulo zimene zingatithandize kuthetsa mikangano m’banja ndi kukhala osangalala.” Asonyezeni nkhani imene yayambira patsamba 18.
Galamukani! Feb.
“Anthu ena amakhulupirira kuti Mulungu amasunga cholakwa chilichonse chimene tachita. Ena amati iye amakhululuka, kaya tchimo lathu likhale lalikulu bwanji. Inu mukuganiza bwanji? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno werengani Machitidwe 3:19.] Nkhani iyi ikufotokoza zinthu zitatu zotchulidwa m’Baibulo zimene tiyenera kuchita kuti Mulungu atikhululukire.” Asonyezeni nkhani imene yayambira patsamba 10.
Nsanja ya Olonda Mar. 1
“Ndikufuna ndimve maganizo anu palemba ili. [Werengani Yohane 3:16.] Kodi munayamba mwadabwapo kuti zingatheke bwanji imfa ya munthu mmodzi kupatsa mwayi anthu ena onse kukhala ndi moyo wosatha? [Yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikufotokoza momveka bwino mmene tingapindulire ndi imfa ya Yesu.”
Galamukani! Mar.
“Kodi mukuganiza kuti zipembedzo zonse ndi zabwino? [Yembekezani ayankhe.] Taonani zimene Baibulo limanena zokhudza kulambira kwa anthu ena. [Werengani Maliko 7:7.] Kodi munthu angadziwe bwanji ngati chipembedzo chikuphunzitsa choonadi osati ‘malangizo a anthu’? Kodi n’zotheka kudziwa choonadi pankhani ya kulambira? Magazini iyi ikuyankha mafunso amenewa.”