Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda Jan. 1
“Kodi mungavomereze kuti izi ndi zoona? [Werengani Yakobe 3:2.] Nkhani iyi ili ndi mfundo zochokera m’Baibulo zotithandiza kupewa kulankhula zinthu zokhumudwitsa anthu apabanja pathu.” Sonyezani nkhani imene yayambira patsamba 10.
Galamukani! Jan.
“Banja lililonse limakumana ndi mavuto. Kodi mukuganiza kuti mwamuna ndi mkazi wake angapeze kuti malangizo odalirika? [Yembekezani ayankhe.] Taonani malangizo abwino awa. [Werengani Aefeso 5:22, 25.] Nkhani iyi ikufotokoza mmene mkazi angasonyezere kuti amagonjera mwamuna wake.” Sonyezani nkhani yomwe yayambira patsamba 28.
Nsaja ya Olonda Feb. 1
“Kodi mukuganiza kuti n’zotheka kukhala ndi mtendere weniweni wam’maganizo masiku ano, ngakhale kuti tikukumana ndi mavuto ambiri? [Yembekezani ayankhe.] Kuganizira za chiyembekezo cham’tsogolo chimene Baibulo limapereka kwathandiza anthu ambiri. [Werengani lemba limodzi la malemba amene agwidwa mawu kapena osagwidwa mawu mu nkhani imene mukugwiritsa ntchito.] Magazini iyi ikufotokoza zimene Baibulo limanena zokhudza kumene anthufe tikuchokera, cholinga cha moyo, ndi zimene zili m’tsogolo mwathu.”
Galamukani! Feb.
“Chifukwa cha kuchuluka kwa chiwawa, anthu ambiri amaona kuti alibe chitetezo. Kodi mukuganiza kuti zinthu zidzasintha? [Yembekezani ayankhe.] Taonani ulosi wosangalatsa uwu m’Baibulo. [Werengani Salmo 37:10.] Magazini iyi ikufotokoza vuto lenileni limene limachititsa chiwawa ndi mmene chidzathetsedwere malingana ndi zimene Baibulo limanena.”