Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda Jan. 15
“Pa zaka zochepa zapitazi, anthu ambiri akhala akuchita chidwi kwabasi ndi nkhani za angelo. Kodi munayamba mwadzifunsapo kuti angelo ndi anthu otani makamaka ndipo kuti amatikhudza bwanji ifeyo? [Asiyeni ayankhe. Kenaka werengani Salmo 34:7.] Magazini iyi ikulongosola zimene Baibulo limanena zokhudza zochita za angelo za kale, za panopo ndi za m’tsogolo.”
Galamukani! Jan.
“Masiku ano n’zotheka kupeza malangizo mwina pa nkhani ina iliyonse. Kodi mukuganiza kuti malangizo onsewo amakhaladi othandiza? [Asiyeni ayankhe. Kenaka werengani 2 Timoteo 3:16.] Magazini ino ya Galamukani! ikulongosola chifukwa chimene tingadalire Baibulo tikafuna nzeru zothandizadi.” Asonyezeni nkhani imene yayambira pa tsamba 18.
Nsanja ya Olonda Feb. 1
“Tonsefe timafunikira ndalama pamoyo wathu. Koma kodi simungavomereze kuti m’pofunika kusamala ndi zimene zalembedwa apa? [Werengani 1 Timoteo 6:10, ndipo asiyeni ayankhe.] Magazini ino ya Nsanja ya Olonda ikutithandiza kudziwa mavuto ena odziwika kwambiri munthu akakhala ndi chuma ndipo ikulongosola mmene tingawapewere.”
Galamukani! Feb.
“Ambirife amene tili ndi achibale ndiponso anzathu okalamba timafuna titadziwa bwinobwino kuti tingawathandize bwanji pa mavuto awo monga anthu achikulire. Kodi si choncho? [Asiyeni ayankhe.] Magazini ino ikufotokoza zinthu zina zimene tingachite kuti anthuwa ukalamba asaumve kuwawa kwambiri. Ikulongosolanso mmene ulosi uwu udzakwaniritsidwire.” Werengani Yobu 33:25.