Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda Jan. 15
“Kodi mukuganiza kuti anthu omwe ali pabanja angapeze kuti malangizo odalirika? [Yembekezani ayankhe.] Taonani amene anayambitsa ukwati. [Werengani Genesis 2:22.] Magazini iyi ikufotokoza za malangizo amene Mulungu anapereka pa udindo wolemekezeka wa mwamuna ndi mkazi.”
Galamukani! Jan.
“Kodi mwaona kuti anthu ambiri amene amadzitcha kuti ndi Akhristu satsatira zimene Yesu anaphunzitsa? [Yembekezani ayankhe.] Mwachitsanzo, ambiri satsatira mawu a Yesu omwe ali pa lemba ili. [Werengani Yohane 13:35.] Nkhani iyi ikulongosola bwino kusiyana kwa zimene Yesu anaphunzitsa ndi zoganiza za anthu ambiri amene amati ndi Akhristu.” Asonyezeni nkhani imene yayambira pa tsamba 18.
Nsanja ya Olonda Feb. 1
“Kodi mukuganiza kuti dera lathu lino likanakhala labwinopo ngati aliyense akanatsatira mawu awa? [Werengani Aefeso 4:25. Ndipo kenako yembekezani ayankhe.] Anthu ambiri amaganiza kuti kunama n’kololeka m’njira zina. Magazini iyi ikufotokoza mmene tingapindulire tikamanena zoona nthawi zonse.”
Galamukani! Feb.
“Zikuoneka kuti m’madera ena, anthu ayamba kusintha maganizo pa nkhani ya kupembedza. Kodi inuyo mukuganiza kuti matchalitchi akuchepa mphamvu? [Yembekezani ayankhe.] Mawu awa a mtumwi Paulo akupereka chifukwa chimene anthu ena anasiyira kukhulupirira chipembedzo. [Werengani Machitidwe 20:29, 30.] Magazini iyi ikusonyeza zimene Baibulo limanena zokhudza tsogolo la Chikhristu.”