Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini
Nsanja ya Olonda Dec. 15
“Chaka chilichonse nyengo ngati ino, anthu ambiri amakumbukira kubadwa kwa Yesu. Kodi mumadziŵa kuti pali zinthu zofunika kwambiri zimene tingaphunzire pankhani ya m’Baibulo ya kubadwa kwa Yesu? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno pitani pa tsamba 5, ndipo ŵerengani 2 Timoteo 3:16.] Nsanja ya Olonda iyi ikutchula zina mwa zinthu zimene tingaphunzirepo.”
Galamukani! Jan. 8
“Ndikukambirana ndi anthu lemba ili la Marko 10:21-23. [Ŵerengani.] Anthu ambiri akaŵerenga lemba ili amaganiza kuti Akristu sayenera kukhala anthu achuma koma amphaŵi. Nanga inu mukuganiza bwanji? [Yembekezani ayankhe.] Galamukani! iyi, pankhani yakuti “Lingaliro la Baibulo,” ikufotokoza zimene Yesu anatanthauza ndi mawu ameneŵa.”
Nsanja ya Olonda Jan. 1
“Nthaŵi zambiri munthu akakhala kuti wokondedwa wake wamwalira kapena wadwala, amafunsa kuti, ‘N’chifukwa chiyani Mulungu amalola zimenezi?’ Mwina munafunsapo funso ngati limeneli. Baibulo limasonyeza kuti Mulungu amawamvera chisoni anthu ovutika. [Ŵerengani Yesaya 63:9a.] Magazini iyi ikufotokoza chifukwa chake tingakhulupirire kuti Mulungu adzathetsa mavuto.”
Galamukani! Jan. 8
“Kodi mukuganiza kuti boma liyenera kupondereza ufulu wa anthu wa kulankhula? [Yembekezani ayankhe.] Bwanji nanga ngati akulankhula ndi anzawo za chipembedzo, monga mmene pakunenera apa? [Ŵerengani Machitidwe 28:30, 31.] Posachedwapa, funso limeneli linakafika ku Khoti Lalikulu ku United States. Tikukupemphani kuŵerenga za nkhaniyi mu Galamukani! iyi.”