Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini
Nsanja ya Olonda Jan. 15
“Anthu ambiri amagwiritsa ntchito mafano polambira. Kodi muganiza kuti zinthu ngati zimenezi zili ndi mphamvu yopulumutsa munthu? [M’yembekezeni ayankhe.] Taonani zimene Mulungu woona adzatichitira. [Ŵerengani Chivumbulutso 21:3, 4.] Amene angachite zimenezi ndi Mulungu weniweni yekha basi. Magazini iyi ikufotokoza kuti ameneyo ndi ndani komanso mapindu amene tingapeze mwa kum’khulupirira.”
Galamukani! Jan. 8
“Kodi simukuvomereza kuti tifunika chakudya chabwino ndi chodalirika kuti titeteze moyo wathu? [M’yembekezeni ayankhe.] Onani zimene Mulungu analonjeza anthu ake kalelo m’nthaŵi za m’Baibulo. [Ŵerengani Levitiko 26:4, 5.] Galamukani! ikufotokoza zinthu zimene zikudetsa nkhaŵa masiku ano pankhani ya zimene timadya. Ikunenanso za nthaŵi imene Mulungu adzatipatsa chitetezo padziko lonse.”
Nsanja ya Olonda Feb. 1
“Anthu ambiri akuda nkhaŵa chifukwa cha kuipa kwa malo. Koma kodi munaganizapo zakuti maganizo angaipenso? [M’yembekezeni ayankhe.] Baibulo limagogomeza kuti ukhondo wa thupi ndi wauzimu n’ngofunika kwambiri. [Ŵerengani 2 Akorinto 7:1.] Ndikhulupirira kuti nkhani imeneyi ikuthandizani kwambiri.”
Galamukani! Jan. 8
“Tonse tikudziŵa za tsokali limene lagwedeza dziko lonse. Kuyambira pamene zimenezi zinachitika, anthu ambiri afuna chilimbikitso ndi chithandizo chachikulu. Nkhani ino mwa zina, ikufotokoza zimene Mboni za Yehova zakhala zikuchita pothandiza anthu opulumuka pa tsoka limeneli ndi anthu othandiza ovulala ndiponso anthu amene abale awo anamwalira pa tsokali.”