Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini
Nsanja ya Olonda Jan. 15
“Chifukwa chakuti masiku ano anthu ambiri sasunga malonjezo, ambiri zimawavuta kudalira munthu aliyense. Kodi mukuganiza kuti pali amene tingadalire malonjezo ake? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno ŵerengani Yoswa 23:14.] Magazini iyi ikusonyeza zimene tingachite kuti tizidalira malonjezo a Mulungu amene analembedwa m’Baibulo.”
Galamukani! Jan. 8
“Tonsefe timalakalaka kuona ana athu akukhala mosangalala komanso zinthu zikuwayendera bwino. Kodi mumaganiza kuti n’chiyani chomwe ana amafunikira kwambiri kuti akhale bwinobwino m’dziko la masiku ano lodzala mavutoli? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno ŵerengani Miyambo 22:6.] Magazini ya Galamukani! iyi ikufotokoza zomwe ana amafunikira ndiponso momwe makolo angakwaniritsire zofunikazo.”
Nsanja ya Olonda Feb. 1
“Ambirife timayesetsa kusamalira thanzi lathu. Komabe, zimene anthu ena ofufuza apeza posachedwapa zikusonyeza kuti moyo wathu umadaliranso zinthu zauzimu. Kodi mukuganiza kuti zimenezi n’zoona? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno ŵerengani Mateyu 5:3.] Magazini iyi ya Nsanja ya Olonda ikufotokoza zimene tingachite kuti tikwaniritse zosoŵa zathu zauzimu.”
Galamukani! Jan. 8
“Padziko lonse, anthu miyandamiyanda akuvutika ndi matenda osiyanasiyana a m’maganizo. Mlengi wathu amawakonda kwambiri anthu ameneŵa. [Ŵerengani Salmo 34:18.] Magazini iyi ikufotokoza mmene odwala angathandizidwire. Komanso ikutchula lonjezo la m’Baibulo loti posachedwapa matenda onse adzathetsedwa.”