Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda Feb. 15
“Nthawi zina, timamva nkhani zonena kuti kwachitika chozizwitsa. [Tchulani chitsanzo.] Anthu ena amakhulupirira nkhani zimenezi. Pamene ena amakayikira. Magazini iyi ikufotokoza ngati zozizwitsa zimene zili m’Baibulo zinachitikadi ndiponso ngati zinthu zimenezi zimachitikanso masiku ano.” Werengani Yeremiya 32:21.
Galamukani! Mar. 8
“Nthawi zakale, Mulungu analamula ana kulemekeza amayi awo ndiponso atate awo. [Werengani Eksodo 20:12.] Kodi muganiza kuti masiku ano amayi akulemekezedwa mmene afunikira? [Yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikufotokoza mavuto amene amayi akukumana nawo m’madera osiyanasiyana ndiponso zimene akuchita kuti athane ndi mavuto amenewo.”
Nsanja ya Olonda Mar. 1
“Kodi muganiza kuti dzikoli likanakhala malo abwino ngati aliyense akanagwiritsa ntchito langizo ili? [Werengani Aroma 12:17, 18. Ndiyeno yembekezani ayankhe.] N’zomvetsa chisoni kuti anthufe nthawi zina timasemphana maganizo. Magazini iyi ikusonyeza mmene kugwiritsira ntchito uphungu wa m’Baibulo kungatithandizire kuthetsa mikangano ndi kukhazikitsanso mtendere.”
Galamukani! Mar. 8
“Chiwerengero cha anthu ofuna magetsi chikukwera chaka chilichonse. Tangoganizani, n’chiyani chingachitike ngati titakhala tsiku limodzi opanda magetsi? [Yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikufotokoza kupita patsogolo komwe kwachitika kuti apeze gwero labwino la mphamvu za magetsi. Ikutchulanso za gwero la mphamvu zonse.” Werengani Yesaya 40:26.