Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 3/05 tsamba 1
  • Kugogomezera Kwambiri Baibulo!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kugogomezera Kwambiri Baibulo!
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
  • Nkhani Yofanana
  • Kwa Owerenga
    Galamukani!—2006
  • Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!—Magazini Apanthaŵi Yake a Chowonadi
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Kodi Yesu Anapereka Lamulo Lotani Lokhudza Kuchita Zinthu ndi Ena?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Gawirani Magazini Amene Amachitira Umboni Choonadi
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
km 3/05 tsamba 1

Kugogomezera Kwambiri Baibulo!

1. Kuchokera pa chiyambi, kodi Nsanja ya Olonda makamaka inakonzedwera ndani, nanga magazini ya The Golden Age inakonzedwera ndani?

1 Pa October 1, 1919, magazini yoyamba ya The Golden Age inatulutsidwa. Inakhala magazini yothandiza kwambiri pa ntchito yolalikira. Chifukwa chiyani? Chifukwa anaipangira anthu onse. Koma sizinali choncho ndi Nsanja ya Olonda, imene kwa zaka zambiri inadziwika monga magazini ya “kagulu ka nkhosa.” (Luka 12:32) Ofalitsa Ufumu analandira magazini yatsopanoyi ndi manja awiri mwakuti kwa zaka zambiri The Golden Age inagawidwa zedi kuposa magazini ya Nsanja ya Olonda.

2. Kodi dzina la magazini ya The Golden Age ndi loti chiyani masiku ano, ndipo kodi cholinga chake chakhala chiyani kuchokera pamene inayamba?

2 Magazini ya The Golden Age inayamba kufalitsidwa n’cholinga chosonyeza anthu kuti mavuto awo onse adzathetsedwa mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Kristu, umene udzadzetsa nthawi yabwino kwambiri kwa anthu. Koma m’kupita kwa nthawi, zambiri zinasintha m’magazini imeneyi ya The Golden Age n’cholinga choti ikwaniritse zofunika panthawiyo. Mu 1937 dzina lake linasinthidwa kukhala Consolation. Ndipo mu 1946 inasinthidwanso kukhala Galamukani!, dzina limene magaziniyi imadziwika nalo panopa.

3. Kodi Galamukani! yakhala magazini yamphamvu pokwaniritsa ulosi uti?

3 Kuchokera pamene inayamba, magazini imeneyi yagwiritsidwa ntchito kwambiri kuchitira umboni umene wakhala ukuperekedwa kuchokera mu 1919. (Mat. 24:14) Komabe poona kuti nthawi yatsala pang’ono kutha, taona kuti ndi bwino kusinthanso zina pa magazini imeneyi ya Galamukani!

4. (a) Kodi munthu afunika kuchitanji ngati akufuna kudzabisika pa “tsiku la mkwiyo wa Yehova”? (b) Malinga ndi Chivumbulutso 14:6, 7, kodi ‘mngelo amene ali kuuluka pakati pa mlengalenga’ akuuza anthu onse kuchita chiyani?

4 Anthu mamiliyoni amakonda kuwerenga Galamukani! chifukwa imakhala ndi nkhani zosiyanasiyana zosakhudzana ndi chipembedzo zomwe zimalembedwa m’njira yosangalatsa kwambiri. Sitikukayikira kuti anthu amene amapezeka pa Chikumbutso chaka chilichonse ndi amene amakonda kuwerenga Galamukani! nthawi zonse. Komabe, ngati munthu akufuna kudzabisika pa “tsiku la mkwiyo wa Yehova,” afunikira thandizo kuti achite zambiri m’malo mongokhala munthu wokonda kuwerenga mabuku athu nthawi zonse.—Zef. 2:3; Chiv. 14:6, 7.

5. (a) Kuyambira ndi Galamukani! ya January 2006, kodi nkhani zake zizikamba kwambiri za chiyani? (b) Kodi ambiri adzafuna kuchita chiyani, ndipo zimenezi zidzakwaniritsa ulosi uti?

5 Pachifukwa chimenechi, kuyambira January 2006, Galamukani! izigogomezera kwambiri Ufumu wa Mulungu. Mosapita m’mbali izilimbikitsa owerenga kuti aziyang’ana m’Baibulo kuti apeze njira imene angathetsere mavuto awo ndipo izifotokoza kwambiri mfundo za m’Baibulo zosonyeza chifukwa chake m’nthawi yathu ino zinthu zikuchitika mmene zikuchitikiramu. Mwanjira imeneyi owerenga azitha kumvetsa bwino zinthu zimene zikuchitika m’nthawi yathu ino ndiponso mwina kuchokera pa zimene awerengazo, angafune kuphunzira zambiri ponena za Yehova.—Zek. 8:23.

6, 7. (a) Kodi Galamukani! iyamba kuthandiza bwanji anthu ambiri kugwiritsa ntchito lemba la 1 Atesalonika 2:13? (b) Kodi Galamukani! izituluka kangati pa mwezi, ndipo kodi kusintha kumeneku kukhudza zinenero zingati?

6 Magazini ya Galamukani! ipitirizabe kukhala ndi nkhani zosiyanasiyana. Koma izigogomezera kwambiri Baibulo. (1 Ates. 2:13) Popeza kuti Nsanja ya Olonda imakhala ndi nkhani zozama za m’Baibulo ndipo Galamukani! izikhala ndi nkhani zambiri za m’Malemba, zikuoneka kuti sipakufunikiranso kupitiriza kutulutsa Galamukani! kawiri pa mwezi. Choncho, kuyambira January 2006, Galamukani! idzayamba kutuluka kamodzi pa mwezi. Zimenezi zidzathandiza kuchepetsa ntchito yokonza, kumasulira, ndi kutumiza mabuku athu.

7 Kusintha kumeneku kudzakhudza pafupifupi theka la zinenero zimene Galamukani! imafalitsidwa. M’zinenero zambiri, Galamukani! imatuluka kamodzi pa mwezi kapena kamodzi pa miyezi itatu iliyonse. Koma sipadzakhala kusintha kwina kulikonse ndi magazini ya Nsanja ya Olonda.

8. Kodi ofalitsa azigwiritsa ntchito bwanji Galamukani! pamodzi ndi Nsanja ya Olonda?

8 Ofalitsa angagawire Galamukani! limodzi ndi Nsanja ya Olonda iliyonse ya mwezi umenewo. Amene akugawira Galamukani! azidzagawira magazini yomweyo mwezi wonse popanda kusintha ulaliki wawo m’kati mwa mwezi monga mmene zikuchitikira panopa.

9. Kodi Galamukani! idzapitirizabe kugwira ntchito yanji?

9 Kuchokera pamene inatulutsidwa koyamba mu 1919, magazini yodziwika kuti The Golden Age, Consolation, ndipo panopa Galamukani!, yathandiza kwambiri pa ntchito yolalikira. Tikupempha Yehova kuti apitirizebe kudalitsa ntchito yogawira magaziniyi imene iyambe kukonzedwa mwatsopano. Ndiponso tikupempha kuti magaziniyi ithandize anthu ambiri “ochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe” kuyembekeza Ufumu wa Mulungu umene ndi wokhawo umene ungawathandize.—Chiv. 7:9.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena