Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 3/95 tsamba 1
  • Kuthandiza Achichepere Athu Kukhala Ofalitsa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuthandiza Achichepere Athu Kukhala Ofalitsa
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
km 3/95 tsamba 1

Kuthandiza Achichepere Athu Kukhala Ofalitsa

1 Kuwonjezera pa thayo lathu la kukhala atumiki a Ufumu, palinso thayo lina limene limagwera awo amene ali ndi mabanja. Atumiki a Ufumu opita patsogolo okhala ndi mabanja, ayenera kuphunzitsa ana awo chifukwa cha thayo lawolo lopatsidwa ndi Mulungu monga makolo. Chaka chilichonse chiŵerengero chabwino cha amene amabatizidwa ali achichepere amene makolo awo anawakulitsa “m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.” (Aef. 6:4) Nzachisoni kunena kuti, ena anyalanyaza thayo limeneli ndi mwaŵi wake, zikumawachititsa chisoni chachikulu. Kodi umenewu ndiwo ungakhale mkhalidwe wa banja lanu? Bwanji ponena za mumpingo wanu, kodi alipo achichepere amene akufunikira chithandizo kuti ayeneretsedwe kukhala ofalitsa osabatizidwa? Makolo ndi akulu afunikira kugwirira ntchito pamodzi kuti afikire chonulirapo chimenechi.

2 Ngakhale kuti kuphunzitsa ana kuli makamaka thayo la makolo, akulu nawonso ali ndi thayo kulinga kwa achichepere mumpingo. Posamalira nkhosa za Mulungu, oyang’anira afunikiranso kuŵeta ana a nkhosa. (1 Pet. 5:1-3) Ha, ndi chitsanzo chabwino koposa chotani nanga chimene Yehova wapereka cha kusamalira ngakhale aang’ono! (Yes. 40:11) Potsatira chitsanzo chimenechi, abusa aang’ono Achikristu ayeneranso kusonyeza chisonkhezero chachikondi kwa achichepere ndi kuwachititsa kumva kukhala mbali ya mpingo.

3 Kufunafuna Ufumu Choyamba: Ngati chinthu china chili choyamba m’moyo wa munthu, chinthucho nchofunika kwambiri. Yesu anati: “Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikane yekha, nanyamule [mtengo wake wozunzirapo, NW] tsiku ndi tsiku, nanditsate ine.” (Luka 9:23) Kukhala wotsatira weniweni wa Yesu ndi kudzikana kumafuna kuti munthu afunefunedi Ufumu choyamba. Chifukwa cha chikhoterero chathu cha kupanda ungwiro cha maganizo ndi mtima kuyambira pakubadwa kumkabe mtsogolo kaamba ka choloŵa cha uchimo, tonsefe tifunikira kulangizidwa kapena kuphunzitsidwa zimene tiyenera kuchita kuti tikondweretse Mulungu. (Gen. 8:21; Aroma 5:12) Tiyenera kuphunzitsidwa kufunafuna Ufumu choyamba, chifukwa chakuti, ngati tisiyidwa patokha, tidzangofunafuna choyamba zokhumba zathu ndi zotisangalatsa. Chotero Yehova wapereka malangizo amene amafika kwa ife kudzera m’Mawu ake ndi kutipatsa chitsogozo choyenera.

4 Yehova analamula anthu ake osankhika, Aisrayeli akale, kuphunzitsa ana awo malamulo ndi malangizo ake. Iwo anafunikira kubwereza ziphunzitsozo panyumba, pamene anali kwina kosakhala kunyumba, pamene anali kupumula ndi pamene anali kugwira ntchito. (Deut. 6:6-9) Chilangizo chimodzimodzicho nchoyenera kwa mabanja lerolino popereka utumiki wawo wopatulika kwa Mulungu. Pamene tiphunzitsidwa kufunafuna Ufumu choyamba, timaphunzira kutenga mathayo. Limodzi la mathayo amenewo ndilo kugaŵana. Kuphunzitsa ana malamulo a Mulungu ndi malangizo ake kungawathandize kukhala olengeza uthenga wabwino ogwira mtima. Lipoti lina losimba za imodzi ya maprogramu a Tsiku la Msonkhano Wapadera lili ndi chokumana nacho ichi: “Atsikana achichepere aŵiri anagwiritsiridwa ntchito kusonyeza kagaŵiridwe ka magazini m’mphindi imodzi. Iwo ndi a misinkhu ya zaka 8 ndi 14. Sikunali kovuta kwa wa zaka 8 chifukwa chakuti ngakhale kunyumba ali wokangalika kwambiri mu utumiki wakumunda. Zimenezi zinasonkhezera ena kuchitapo kanthu amene anaganiza kuti nkovuta kuphunzitsa ana m’masiku ano otsiriza.”

5 Kugaŵana: Panopa sitifuna kutayira nthaŵi kwambiri pa kufotokoza tanthauzo la kugaŵana m’lingaliro la zinthu zakuthupi, kumene kuli kofunikanso kaamba ka chimwemwe chenicheni. (Mac. 20:35) Mfundo yathu ndi ya kugaŵana mwa kupatsa ena mwaŵi wa kukhala ndi chiyembekezo chimene Akristu ali nacho cha Ufumu wa Mulungu. Umodzi wa mikhalidwe yabwino koposa imene kholo lingaphunzitse mwana wake ndiwo chikhumbo cha kugaŵana uthenga wabwino wa Ufumu ndi ena. Kuyambira paubwana ana angaphunzitsidwe kukhala ndi phande m’kulankhula ndi ena za ‘uthenga wabwino wa Ufumu.’—Mat. 24:14.

6 Chimenechi chimachititsa thayo la makolo Achikristu kukhala lofunika kwambiri pa kuphunzitsa ana awo kukhala ndi phande mu utumiki wopatulika umenewu. Utumiki woterowo umafalitsa chidziŵitso chonena za Kristu, chimene chimachititsa chisangalalo chachikulu kwa oŵerengeka, koma chimene chimakanidwa ndi ambiri. Makolo ali ndi mwaŵi ndi thayo la kuyamba kuphunzitsa ana awo akali aang’ono kuti akhale okonzekera ndi okonzekeretsedwa kukhala ndi phande mu utumiki wopatulika umenewu, akumafalitsa kwa ena uthenga wonena za Kristu ndi Ufumu. Ana amafunikira chithandizo chachikulu kuti azindikire zimenezo, ngakhale kuti ambiri amaona uthenga waulemerero wochokera kwa Mulungu kukhala wodzetsa imfa, alengezi achichepere a uthenga wabwino sayenera kutaya chisangalalo ndi changu chawo. Safunikira ngakhale kufooketsa dzanja ndi kuleka kukhala ndi phande m’kupereka utumiki wopatulika kwa Yehova.—1 Akor. 9:16, 17.

7 Kuti aphunzitse moyenera, tate kapena mayi, kapena onse aŵiri pamene kuli kotheka, ayenera kukhala limodzi ndi ana awo. Ayenera kukhala ndi phande mu utumiki wopatulika monga banja. Nzoona kuti, kuti munthu akhale ndi phande poyera ndi ofalitsa ena m’kulalikira uthenga wabwino, afunikira choyamba kuyeneretsedwa monga wofalitsa wosabatizidwa. Komabe, ponena za ana aang’ono, palibe choletsa kwa makolo kugwira nawo ntchito mu utumiki wakumunda ngakhale kuti sali ofalitsa osabatizidwa.

8 Kugaŵana uthenga wabwino ndi ena kumeneku kuli ndi zotulukapo zopindulitsa, kuwonjezera pa kupatsa munthu chikhutiro cha kudziŵa kuti akuchita chimene Yehova walamula. Kumapatsa ana a munthu zonulirapo zoyenera zozikalimira m’moyo. Pamene kuli kwakuti dziko lonse likufunafuna chikhutiro, mabanja aumulungu mumpingo Wachikristu akuchipeza pafupi, ngati angachitenge. Pali mbali zambiri zopatsa chikhutiro. (Aef. 5:15, 16) Ndithudi, tiyeni tonsefe chaka chautumiki chino tiike chonulirapo cha kuthandiza achichepere athu kukhala ofalitsa.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena