Misonkhano Yautumiki ya March
Mlungu Woyambira March 6
Mph. 13: Zilengezo za pamalopo ndi Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu Waufumu. Kambitsiranani Bokosi la Mafunso.
Mph. 15: “Kuthandiza Achichepere Athu Kukhala Ofalitsa.” Mafunso ndi mayankho. Limbikitsani makolo kupanga programu yothandizira ana awo kukhala ofalitsa.
Mph. 17: “Thandizani Achichepere Kuyamikira Buku lakuti Mafunso Achichepere Akufunsa.” Longosolani mfundo zazikulu. Pemphani omvetsera kusimba zokumana nazo zimene anasangalala nazo pogwiritsira ntchito kapena pogaŵira buku lakuti Mafunso Achichepere Akufunsa. Limbikitsani onse kukhala ndi maganizo abwino pogaŵira bukulo, popeza kuti limafotokoza za mikhalidwe imene ilipo imene imakhudza achichepere. Khalani ndi chitsanzo cha ulaliki umodzi kapena aŵiri.
Nyimbo Na. 31 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira March 13
Mph. 10: Zilengezo za pamalopo. Fotokozani mwachidule za bokosi lakuti “Chikumbutso kwa Mlembi ndi Woyang’anira Utumiki.” Lipoti la Maakaunti.
Mph. 15: “Uthenga wa Ufumu wa Panthaŵi Yake Woyenera Kufalitsidwa pa Dziko Lonse.” Nkhani yokambidwa ndi mkulu. Gogomezerani kufunika kwa ntchito ikudzayo mu April ndi May. Limbikitsani onse, kuphatikizapo atsopano, kukonzekera kudzakhala ndi phande mokwanira. Tikuyembekezera kuti achichepere ambiri adzakhala pakati pa ofalitsawo.
Mph. 20: “Msonkhano Wachigawo wa ‘Atamandi Achimwemwe’ wa 1995 wa Mboni za Yehova.” Kukambitsirana kwa mafunso ndi mayankho ndime 1-10 kochititsidwa ndi mlembi wa mpingo.
Nyimbo Na. 36 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira March 20
Mph. 15: Zilengezo za pamalopo. Tsiku la Magazini Lapadera la April 1, 1995. Longosolani malingaliro otsatirawa ogaŵirira magazini kunyumba ndi nyumba: Khalani omwetulira mwaubwenzi. Khalani wosangalala. Lankhulani modekha. Kambitsiranani nkhani imodzi m’magazini amodzi. Perekani magazini m’manja mwa mwininyumba. Mudziŵitseni kuti mudzabweranso ndi makope otsatira. Nenani mawu omaliza abwino pamene magazini akanidwa. Khalani ndi cholembapo okondwerera ndi zogaŵira. Pomaliza, khalani ndi chitsanzo cha ulaliki umodzi wachidule kapena aŵiri a kugaŵira makope a magazini atsopano. Malizani ndi kupenda bokosi lakuti “Kodi Tinachita Motani m’October?”
Mph. 15: Zosoŵa za pamalopo. Kapena nkhani yakuti: “M’kamwa mwa Makanda,” mu Nsanja ya Olonda ya January 1, 1995, masamba 24-6.
Mph. 15: “Thandizani Achichepere mwa Kupanga Maulendo Obwereza Ogwira Mtima.” Longosolani mfundo zazikulu, ndiyeno chitirani chitsanzo ulendo wobwereza umodzi kapena aŵiri.
Nyimbo Na. 52 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira March 27
Mph. 5: Zilengezo za pamalopo.
Mph. 12: “Chochitika Chofunika Koposa m’Mbiri ya Anthu.” Kambitsiranani ndi omvetsera. Longosolani makonzedwe a pamalopo a Chikumbutso. Fotokozani chifukwa chimene tiyenera kuitanira okondwerera ndi kuwathandiza kupezekapo.
Mph. 23: “Kufeŵetsa Zinthu pa Msonkhano.” Kukambitsirana kwa mafunso ndi mayankho ndime 1-15.
Mph. 5: Kugaŵira sabusikripishoni ya Nsanja ya Olonda mu April. Sonyezani chitsanzo cha chogaŵira. Kumbutsani ofalitsa onse kunyamula masilipi a sabusikripishoni m’zola zawo za mu umboni.
Nyimbo Na. 176 ndi pemphero lomaliza.