Thandizani Achichepere mwa Kupanga Maulendo Obwereza Ogwira Mtima
1 Kungoŵerenga buku lakuti Achichepere Akufunsa sikokwanira. Kuti munthu apindule kwambiri, ayenera kumvetsetsa zolembedwamo. Kugaŵira buku kwangokhala chiyambi chabe cha kupanga ophunzira. Titangopeza okondwerera amene afuna kumvetsera, tiyenera kubwererako mwamsanga kukawathandiza kuphunzira zambiri. Kodi tingalankhule za chiyani pa ulendo wathu wobwereza?
2 Ngati munakambitsirana Salmo 119:9 pa ulendo woyamba, mungapitirize mwa kunena kuti:
◼ “Pamene ndinali kuno tsiku lija, tinaŵerenga Salmo 119:9, ndipo tinathandizidwa kuona mmene achichepere angapezere chitsogozo choyenera. Kodi muganiza kuti achichepere angapeze kuti chitsogozo chenicheni lerolino? [Yembekezani yankho. Ŵerengani Yeremiya 10:23.] Monga momwe mungaonere, Mulungu sanafune kuti munthu atsogoze zochita zake. Kuyesa kuchita zimenezo popanda thandizo la Mulungu ndiko kwachititsa mavuto ochuluka a achichepere amene tikuona lerolino. Mawu a Mulungu, Baibulo, ndilo buku lokha limene limapereka chitsogozo chenicheni.” Tsegulani patsamba 319 m’buku lakuti Achichepere Akufunsa, ndipo kambitsiranani Salmo 46:1 m’ndime yomaliza. Fotokozani chifukwa chake tiyenera kuika chidaliro chathu chonse mwa Mulungu ndi mapindu a kuphunzira Baibulo.
3 Ngati munakambitsirana za chisonkhezero cha mabwenzi pa ulendo wanu woyamba, mungayambe kukambitsirana motere:
◼ “Tsiku lija tinakambitsirana za chisonkhezero cha mabwenzi ndi mmene achichepere angalimbanirane nacho. Miyambo 29:25a imati: “Kuwopa anthu kutchera msampha.” Lerolino, chikhumbo chofuna kuvomerezedwa ndi mabwenzi chachititsa achichepere ambiri kuswa miyezo yaumulungu. Iwo mopanda nzeru asankha mabwenzi oipa ndipo zimenezi zachititsa ambiri kusuta fodya, kuba, kuchita dama, chiwawa, ndi nsautso. Baibulo pa 1 Akorinto 15:33 limati: ‘Musanyengedwe; mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.’ Kodi muganiza kuti nchiyani chimene chingathandize achichepere kupeŵa misampha yotero? [Yembekezani yankho.] Achichepere ambiri apindula mwa kutsatira Miyambo 29:25b.” Ŵerengani lembalo ndi kukambapo pa chitsanzo cha Debbie m’ndime 1 patsamba 80. Malizani mwa kusonyeza mmene phunziro la mlungu ndi mlungu lingakhalire lopindulitsa.
4 Ngati munasiya trakiti lakuti “Moyo m’Dziko Latsopano Lamtendere”:
◼ Mungasonyeze chithunzi patsamba loyamba ndiyeno nkuŵerenga ndime 1 pakamutu kakuti “Moyo m’Dziko Latsopano la Mulungu.” Ndiyeno nenani kuti: “Ngati mufuna kukhala m’dziko longa limeneli, pali chinthu chofunika chimene tiyenera kuchita.” Ŵerengani ndime yomaliza, ndi kugaŵira buku lakuti Achichepere Akufunsa.
5 Mwina mungafune kuyesa zotsatirazi kuti muyambitse kukambitsirana za m’Malemba:
◼ Sonyezani chithunzi chili patsamba loyamba la trakitilo “Moyo m’Dziko Latsopano Lamtendere,” ndi kufotokoza: “Mtundu wa anthu udzasangalala ndi mikhalidwe imeneyi pamene chifuniro cha Mulungu chichitidwa pa dziko lapansi monga kumwamba. Komabe, ena amada nkhaŵa kuti mikhalidwe yoipa idzakhalakonso. Zimenezo sizidzatheka chifukwa chakuti oipa onse adzachotsedwa.” Ŵerengani Salmo 37:29. Pemphani mwini nyumba kugwiritsira ntchito mwaŵi wa programu yathu ya phunziro la Baibulo kuti aphunzire zambiri. Sonyezani phindu la kuphunzira buku lakuti Achichepere Akufunsa.
6 Popeza kuti cholinga chathu ndicho kuyambitsa maphunziro a Baibulo, tifunikira kupanga maulendo obwereza ogwira mtima. Patulani nthaŵi yake, ndipo konzekerani bwino pasadakhale. Mwa njira imeneyi tingathandizedi oona mtima.—1 Tim. 2:3, 4.