Kodi Tinachita Motani m’October?
Kunali kosangalatsa chotani nanga kuona ofalitsa ambiri m’ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa m’October. Tinali ndi ofalitsa 32,869 amene anachitira lipoti utumiki wawo wakumunda, chiwonjezeko cha 3,598 kuposa chaka chatha. Tinachititsa maphunziro a Baibulo okwanira 27,299, amene anachuluka ndi 3,903 kuposa chaka chatha. Inde, oona mtima akupitiriza kulabadira uthenga wabwino wa Ufumu, ndipo nkosangalatsa chotani nanga kuwathandiza iwo. Motero, tikukulimbikitsani kupitiriza kutumiza malipoti a utumiki wakumunda ku Sosaite panthaŵi yake. Ofalitsa mmodzi ndi mmodzi ayeneranso kukumbutsidwa za kuona kufunika kwa kupereka lipoti lawo la utumiki wakumunda kumpingo kumapeto kwa mwezi uliwonse. Mlembi ayenera kukumbukira nthaŵi zonse kupatsa ochititsa Phunziro Labuku Lampingo maina a ofalitsa amene sanapereke malipoti awo. Chimenechi chiyenera kuchitika mwezi uliwonse.