Kodi Muyenera Kukhala Anthu Otani?
1 Nthaŵi ya kuŵerengera mlandu kwa anthu onse yayandikira. Baibulo limatcha nthaŵiyo “tsiku la Yehova.” Ndi nthaŵi imene chiweruzo chaumulungu chidzaperekedwa kwa anthu oipa; Ilinso nthaŵi ya chipulumutso kwa olungama. Anthu onse amoyo panthaŵiyo adzaŵerengeredwa mlandu pa njira imene anagwiritsira ntchito moyo wawo. Poganizira zimenezo, Petro akudzutsa funso lofuna kudzipenda nalo: “Muyenera inu kukhala anthu otani nanga”? Iye akugogomezera kufunika kwa ‘mayendedwe opatulika, ndi [ntchito za kudzipereka kwaumulungu, NW ], ndi kukumbukira kufulumira kwa kudza kwake kwa tsiku la Mulungu,’ limodzinso ndi kufunika kwa kukhala ‘opanda banga ndi opanda chilema, ndi mumtendere.’—2 Pet. 3:11-14.
2 Mayendedwe Opatulika ndi Ntchito za Kudzipereka Kwaumulungu: Mayendedwe opatulika amaphatikizapo ntchito zabwino zimene zimasonyeza ulemu pa zitsogozo za Baibulo. (Tito 2:7, 8) Mkristu ayenera kupeŵa mayendedwe a dziko amene amasonkhezeredwa ndi zikhumbo zakuthupi zadyera.—Aroma 13:11, 14.
3 “Kudzipereka Kwaumulungu” kumamasuliridwa kukhala “kukhulupirika kwa Mulungu kochokera mumtima wosonkhezeredwa ndi kuyamikira mikhalidwe yake yabwino.” Changu chathu cha utumiki chili njira yapadera imene timasonyezera mkhalidwe umenewu. Cholinga chathu polalikira sindicho kungofuna kukwaniritsa thayo; chimasonkhezeredwa ndi kukonda kwathu Yehova. (Marko 12:29, 30) Posonkhezeredwa ndi chikondi choterocho, timaona utumiki kukhala njira yabwino yosonyezera kudzipereka kwathu kwaumulungu. Popeza kuti kudzipereka kwathu kuyenera kukhala kosalekeza, kukhala kwathu ndi phande m’ntchito yolalikira kuyeneranso kukhala kosalekeza. Kuyenera kukhala mbali yaikulu ya zochita zathu za mlungu ndi mlungu.—Aheb. 13:15.
4 ‘Kukumbukira kufulumira kwa kudza kwa’ tsiku la Yehova kumatanthauza kuliika pafupi m’malingaliro athu a tsiku ndi tsiku, kusaliiŵala konse. Kumatanthauza kuika patsogolo zinthu za Ufumu m’moyo wathu.—Mat. 6:33.
5 Opanda Banga, Opanda Chilema, ndi Mumtendere: Monga mbali ya khamu lalikulu, ‘tatsuka zovala zathu ndi kuziyeretsa m’mwazi wa Mwanawankhosa.’ (Chiv. 7:14) Motero, kukhala “[w]opanda banga” kumatanthauza kuti tiyenera kutetezera zolimba miyoyo yathu yoyera ndi yopatuliridwa kuti isaipitsidwe ndi zodetsa za dzikoli. Timakhala “opanda chilema” mwa kusalola zofuna zakuthupi kulemaza umunthu wathu Wachikrsitu. (Yak. 1:27; 1 Yoh. 2:15-17) Timasonyeza kuti tikukhala “mumtendere” mwa kusonyeza “mtendere wa Mulungu” m’zochita zathu zonse ndi ena.—Afil. 4:7; Aroma 12:18; 14:19.
6 Ngati tidzitetezera bwino lomwe ku kuipitsidwa ndi dziko, ‘sitidzafanizidwa konse ndi makhalidwe a pansi pano,’ amene atsutsidwa ndi Yehova. M’malo mwake, ntchito zathu zabwino zidzathandiza ena kuona kusiyana kwa “pakati pa iye wotumikira Mulungu ndi iye wosamtumikira.”—Aroma 12:2; Mal. 3:18.
7 Ambirife tinapezeka pa Msonkhano Wachigawo wa “Atamandi Achimwemwe,” ndipo mosakayikira chakudya chauzimu chotsitsimula chakulitsa chikhumbo chathu cha kusonyeza kudzipereka kwathu kwaumulungu. Atsopano ambiri ali ndi chikhumbo chimodzimodzi. Tingakhale dalitso kwa iwo mwa kuwathandiza kukhala ndi phande mu utumiki wakumunda mu September.
8 Pamene tisunga ‘ntchito zabwino,’ dzina la Yehova limalemekezedwa, mpingo umalimbikitsidwa, ndipo ena amapidula. (1 Pet 2:12) Tikhaletu anthu a mtundu wotero.