Kodi Tinachita Motani mu April?
Lipoti lathu likusonyeza kupita patsogolo kwabwino pa kugwira ntchito ndi changu. Kuchokera pa chiŵerengero cha ofalitsa 34,983 m’March, tinawonjezeka kufika pa chiŵerengero chapamwamba chatsopano cha 36,171 m’April! Kunali kosangalatsa kuona anthu 545 akubatizidwa mu April. Kunali kwabwino makamaka kuona chiwonjezeko cha maola otheredwa m’munda, magazini ogaŵiridwa, maulendo obwereza amene anapangidwa ndi maphunziro a Baibulo amene anachititsidwa poyerekezera ndi mwezi umodzimodziwo chaka chathachi. Zilidi bwino kwambiri! Kunalidi koyamikirika kuti ambiri anaona kufunika kwa kulimbikira mwamphamvu kudziŵikitsa poyera dzina la Yehova ndi Ufumu wake.
Kodi tingathandize anthu owonjezereka kupeza moyo mwa kuwongolera phande lathu mu utumiki wakumunda? Tigwiritsiretu ntchito nthaŵi mwanzeru m’miyezi ikudzayi kotero kuti tilemekeze Yehova Mulungu mwa kupulumutsa miyoyo yowonjezereka. Timalimbikitsidwa kwambiri ndi umboni wochuluka umenewu wa dalitso la Yehova pa zoyesayesa zathu za ‘kupanga ophunzira’ monga mmene tinalamulidwa ndi Yesu. Kodi tili ndi chifukwa chokhalira ndi chiyembekezo kuti Yehova adzatidalitsa ndi ziwonjezeko zina za ofalitsa? Inde, pakali anthu oona mtima ambiri amene akufuna kutumikira Yehova ndi amene amamvetsera ku ulaliki wathu. Ameneŵa amaphatikizapo zikwi za ana ndi achinyamata amene amagwirizana ndi mipingo yathu, koma amene sakugawanamo mu utumiki wapoyera, ndipo sakuŵerengedwabe monga ofalitsa. Iwo afunikira thandizo lathu.