Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu September: Tidzagwiritsira ntchito buku la Kukhala ndi Moyo Kosatha, ndipo tiyenera kuyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba. Ngati mpingo wanu ulibe mabuku a Kukhala ndi Moyo Kosatha mu sitoko, chonde musawaode ku Sosaite popeza salinso mu sitoko ku ofesi ya nthambi. Pamenepo mungagwiritsire ntchito buku la Kulambiridwa m’malo mwake. October: Masabusikripishoni a Galamukani! kapena Nsanja ya Olonda kapena zonse ziŵiri. November: Gaŵirani buku la Kukhala ndi Moyo Kosatha pamkupiti wapadera. Mipingo imene ilibe buku limeneli iyenera kugaŵira New World Translation ndi buku lakuti Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? CHIDZIŴITSO: Mipingo imene siinaodebe zinthu zamkupiti zotchulidwa pamwambazo iyenera kutero pa fomu yawo ya Literature Request (S-AB-14) yotsatira ya mwezi ndi mwezi. Komabe, mabuku onse a mkupiti wapadera wa m’July, August, September, November 1995, January ndi February 1996 tsopano atumizidwa ku mipingo. Chotero, mipingo siiyenera kuoda mabuku a Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi ndi Kupangitsa Moyo Wanu wa Banja Kukhala Wachimwemwe pafomu yawo ya Literature Request (S-AB-14) popeza kuti Sosaite ilibe alionse mu sitoko.
◼ Woyang’anira wotsogoza kapena winawake woikidwa ndi iye ayenera kuŵerengera maakaunti a mpingo pa September 1 kapena mwamsanga pambuyo pake. Lengezani ku mpingo mutachita zimenezi.
◼ Ofalitsa omwe akukonzekera kukhala apainiya othandiza mu October ayenera kupereka mwamsanga zofunsira zawo. Zimenezi zidzalola akulu kupanga makonzedwe ofunika a mabuku ndi ndime.
◼ Akulu akukumbutsidwa kutsatira malangizo operekedwa pamasamba 21-3 a Nsanja ya Olonda ya April 15, 1991, onena za munthu aliyense wochotsedwa kapena wodzilekanitsa amene angafune kubwezeretsedwa.