Kudzipereka Ife Eni Mwaufulu Kuchita Ntchito Iliyonse Yabwino
1 Chofalitsa china cha dziko chinati ponena za Mboni za Yehova: “Kuli kovuta kupeza anthu a gulu lina lililonse amene amagwira ntchito za chipembedzo chawo molimbika monga Mboni.” Kodi nchifukwa ninji Mboni za Yehova zimagwira ntchito molimbika chotero limodzi ndi mzimu wodzipereka mwaufulu?
2 Chifukwa china nchakuti zimalingalira kwambiri za kuchepa kwa nthaŵi. Yesu anazindikira kuti anali ndi nthaŵi yochepa yomalizira ntchito yake pa dziko lapansi. (Yoh. 9:4) Pamene Mwana wolemekezedwayo wa Mulungu akupitiriza kulakika pakati pa adani ake lerolino, anthu a Yehova amazindikira kuti ali ndi nthaŵi yochepa yochitira ntchito yawo. Motero, amadziperekabe iwo eni mwaufulu kuchita utumiki wopatulika. (Sal. 110:1-3) Popeza kuti pakufunikira antchito owonjezereka pantchito yakututa, iwo sangasiye changu chawo. (Mat. 9:37, 38) Chifukwa chake, amayesetsa kutsanzira Yesu, amene anapereka chitsanzo changwiro cha kukhala wodzipereka ndi wakhama pantchito yake.—Yoh. 5:17.
3 Chifukwa chinanso chimene Mboni za Yehova zimagwirira ntchito ndi mtima wonse kwa Yehova nchakuti gulu lawo la padziko lonse nlosiyana ndi magulu ena onse. Magulu akudziko achipembedzo kwenikweni amafuna nthaŵi ndi kuyesayesa kochepa kwa anthu awo. Zimene amakhulupirira zimakhudza moyo wawo wa tsiku ndi tsiku pang’ono chabe ngati zimatero nkomwe, ndi zochita zawo ndi ena, kapena ntchito zawo m’moyo. Posoŵa mphamvu yosonkhezera ya chikhulupiriro choona, iwo aumirira kuti abusa awo ‘anene kwa iwo zinthu zamyaa,’ zikumawapatsa chitsimikizo chakuti kuyesayesa kwawo kwachiphamaso kuli kokwanira. (Yes. 30:10) Atsogoleri awo achipembedzo ayanja zimenezo mwa ‘kuyabwa m’khutu mwawo,’ akumafesa mzimu wa mphwayi ndi ulesi wauzimu.—2 Tim. 4:3.
4 Pali kusiyana kotani nanga ndi anthu a Yehova! Zilizonse zokhudza kulambira kwathu zimafuna kuyesayesa, khama, ndi ntchito. Tsiku lililonse ndi pa zonse zimene timachita, timatsatira zimene timakhulupirira. Pamene kuli kwakuti choonadi chimatipatsa chimwemwe chachikulu, icho chimafuna “[kulimbikira, NW ] kwambiri” kuti tikwaniritse zimene chimafuna. (Yerekezerani ndi 1 Atesalonika 2:2) Kungosamalira mathayo a moyo wa tsiku ndi tsiku kumatanganitsa anthu ochuluka. Komabe, sitimalola zosamala za moyo zimenezi kutiletsa kuika zinthu za Ufumu pa malo oyamba.—Mat. 6:33.
5 Ntchito yathu mu utumiki wa Yehova ili yopindulitsa ndi yofulumira kwambiri kwakuti timasonkhezereka ‘kuombola’ nthaŵi pa ntchito zina ndi kuigwiritsira ntchito bwino lomwe pa zinthu zauzimu. (Aef. 5:16, NW) Podziŵa kuti kudzipereka kwathu kwaumulungu ndi mzimu wathu wofunitsitsa zimakondweretsa Yehova, tili ndi chifukwa chachikulu koposa chopitirizira kugwiritsa ntchito. Pokhala ndi madalitso ochuluka amene tikulandira tsopano ndi chiyembekezo cha moyo wa mtsogolo, cholinga chathu ndicho kupitiriza ‘kugwiritsa ntchito ndi kuyesetsa’ kaamba ka zinthu za Ufumu.—1 Tim. 4:10.
6 Kudzipereka ndi Mzimu Wodzimana: Anthu ochuluka lerolino amaika pa malo oyamba zinthu zakuthupi kuposa china chilichonse. Amaganiza kuti ali ndi zifukwa zabwino zosumikira maganizo pa zimene adzadya, kumwa, kapena kuvala. (Mat. 6:31) Pokhala osakhutira ndi zofunika zokha, iwo amasonkhezeredwa ndi cholinga cha kukhala ndi moyo wabwino kwambiri tsopano ndi ‘kukhala ndi chuma chambiri chosungika kufikira zaka zambiri; kuti apumuletu, nadye, namwe, nakondwere.’ (Luka 12:19) Opita kutchalitchi ambiri amaganiza kuti changu chimene chipembedzo chawo chimafuna kuti asonyeze chimawalanda ufulu wawo. Amaipidwa ndi kuuzidwa za kusiya kapena ngakhale kuchepetsako ntchito zakuthupi kapena kulekeratu chinthu china chokondweretsa. Pokhala ndi lingaliro la kufuna za iwo okha, kukhala ndi mzimu wodzimana kuli maloto, kosatheka.
7 Nkhani imeneyi timaiona mosiyana. Mawu a Mulungu akweza kulingalira kwathu kwakuti timaganiza zimene Mulungu amaganiza osati zimene anthu amaganiza. (Yes. 55:8, 9) Tili ndi zonulirapo m’moyo zimene ziposa zinthu zathupi. Kutsimikizira kuyenera kwa ulamuliro wa Yehova ndi kuyeretsedwa kwa dzina lake ndizo nkhani zofunika koposa m’chilengedwechonse. Nkhani zimenezi nzazikulu kwambiri kwakuti amitundu onse “ali chabe pamaso pa iye” mutawayerekezera ndi zimenezo. (Yes. 40:17) Zilizonse zotichititsa kukhala ndi moyo mwanjira imene imanyalanyaza chifuniro cha Mulungu tiyenera kuziyesa kupusa.—1 Akor. 3:19.
8 Chotero pamene kuli kwakuti zinthu zina zakuthupi zili zofunika ndipo zinanso zimathandiza pochita ntchito zathu za Ufumu, timazindikira kuti zimenezi kwenikweni sindizo “zinthu zofunika kwambiri.” (Afil. 1:10, NW ) Timatsatira mzimu wa pa 1 Timoteo 6:8 pochepetsa kufunafuna kwathu zinthu zakuthupi ndi poyesayesa mwanzeru kusumika mitima yathu pa “zinthu zosaoneka zili zosatha.”—2 Akor. 4:18.
9 Pamene tiganiza kwambiri zimene Mulungu amaganiza, nkhaŵa yathu ya zinthu zakuthupi imachepa. Pamene tilingalira zimene Yehova watichitira kale ndi madalitso abwino kwambiri amtsogolo amene walonjeza, timafuna kupereka kalikonse kamene iye atipempha. (Marko 10:29, 30) Tili ndi moyo chifukwa cha iye. Pakadapanda chifundo chake ndi chikondi, sitikadakhala ndi moyo tsopano ngakhalenso mtsogolo. Timakakamizika kudzipereka ife eni, pakuti zilizonse zimene timachita mu utumiki wake ‘ndi zimene tiyenera kuchita.’ (Luka 17:10) Chilichonse chimene tipemphedwa kumbwezera Yehova, timachipereka mokondwera, podziŵa kuti ‘tidzatuta mooloŵa manja.’—2 Akor. 9:6, 7.
10 Antchito Aufulu Akufunikira Tsopano: Kuyambira pachiyambi chake, mpingo Wachikristu unaloŵa m’nyengo ya ntchito yochuluka. Umboni wokwana unayenera kuperekedwa Yerusalemu asanapasulidwe mu 70 C.E. Panthaŵiyo ophunzira a Yesu anali “[otanganitsidwa kwambiri, NW ] ndi mawu.” (Mac. 18:5) Kufutukuka kofulumira kumeneko kunafuna kuti alaliki owonjezereka ndi abusa aluso aphunzitsidwe ndi kuti athandize. Panafunikira amuna odziŵa kuchita ndi akuluakulu aboma limodzi ndi amuna okhoza kuyang’anira kusonkhanitsidwa ndi kugaŵiridwa kwa zinthu zakuthupi. (Mac. 6:1-6; Aef. 4:11) Pamene kuli kwakuti angapo anatumikira moonekera kwambiri, ochuluka anakhalabe osadziŵika. Koma onsewo ‘anayesetsa,’ akumagwira ntchito pamodzi ndi mtima wonse kuti amalize ntchitoyo.—Luka 13:24.
11 Ngakhale kuti panalibe kufunikira kwakukulu kwa kuchita ntchito mwachangu pamlingo wa padziko lonse m’zaka mazana ambiri zotsatira, ntchito yaikulu ya Ufumu inayamba pamene Yesu anatenga mphamvu yake ya Ufumu mu 1914. Poyamba, ndi oŵerengeka okha amene anazindikira kuti m’kupita kwa nthaŵi padzafunikira antchito ochuluka kwambiri osamalira zinthu za Ufumu, zikumafuna thandizo la amtima wofunitsitsa la mamiliyoni ambiri m’maiko onse padziko.
12 Lerolino gulu lili lotanganitsidwa kwambiri ndi mapulojekiti ambiri osiyanasiyana amene akufuna ndalama zochuluka kwa ife. Ntchito ya Ufumu ikupita patsogolo mofulumira kwambiri. Kufulumira kwa nthaŵi zathu kumatisonkhezera kuyesetsa ndi kugwiritsira ntchito chuma chathu chilichonse kuchitira ntchito yomwe ilipo. Popeza kuti mapeto a dongosolo lonse loipa la zinthu ayandikira kwambiri, tikuyembekezera ntchito yochuluka kwambiri mtsogolomu. Mtumiki aliyense wodzipatulira wa Yehova akupemphedwa kudzipereka iye mwini mwaufulu pantchito yakututa yofulumirayo.
13 Kodi Tiyenera Kuchitanji? Tikhoza kunenadi kuti pali ‘zochuluka mu ntchito ya Ambuye.’ (1 Akor. 15:58) M’magawo ambiri minda yacha, koma antchito ali oŵerengeka. Tikupemphedwa kuchita mbali yathu osati chabe mwa kuchitira bwino lomwe umboni m’gawo lathu lonse komanso mwa kulandira chiitano cha kukatumikira kumene kusoŵa kuli kokulirapo.
14 Nkoyamikirika kuona Mboni kumbali zonse za dziko zikudzipereka zokha mwaufulu kuchita ntchito zina. Kumeneku kungakhale kudzipereka pantchito yomanga nyumba zolambirira, kutumikira pamisonkhano yaikulu, ndi kuthandizira kupereka thandizo panthaŵi ya tsoka kapena kuyeretsa Nyumba yawo Yaufumu nthaŵi zonse. Ponena za mbali yomalizirayi, tifunikira nthaŵi zonse kutsimikizira kuti Nyumba Yaufumu yasiyidwa yoyera ndi yadongosolo msonkhano uliwonse utatha. Kuchita ntchito zimene zingayesedwe zapansi kumasonyeza kuti tikumvetsa bwino mawu a Yesu pa Luka 16:10: “Iye amene akhulupirika m’chaching’onong’ono alinso wokhulupirika m’chachikulu; ndipo iye amene ali wosalungama m’chaching’onong’ono alinso wosalungama m’chachikulu.”
■ Kuchirikiza Ntchito za pa Mpingo: Pamene kuli kwakuti mpingo uliwonse umatumikira monga mbali ya gulu lonse ndipo umalandira malangizo kwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” wapangidwa ndi ofalitsa Ufumu mmodzi ndi mmodzi. (Mat. 24:45) Zimene umachita zimadalira kwambiri pa mlingo wa zimene Mboni iliyonse ili yokonzekera kuchita. Mpingo umayesayesa kuti uthenga wabwino ulalikidwe m’gawo lake, kupanga ophunzira atsopano, ndiyeno kuwalimbitsa mwauzimu. Aliyense wa ife ayenera kuchirikiza ntchito imeneyi. Ndiponso tingadziikire zonulirapo za phunziro laumwini, kutengamo mbali kwatanthauzo m’misonkhano, ndi kuthandiza ena osoŵa mumpingo. Ntchito zimenezi zimatipatsa mwaŵi wabwino wochuluka wosonyezera chifuno chathu.
■ Kutsogolera kwa Amene Ali m’Malo Auyang’aniro: Yehova waikiza uyang’aniro wa mpingo uliwonse pa akulu oikidwa. (Mac. 20:28) Amuna ameneŵa anakalimira kuti ayenerere mathayo ameneŵa. (1 Tim. 3:1) Tinene kuti abale onse mumpingo akhoza mwa njira ina yake kuyenerera mathayo okulirapo. Abale ambiri akukula mwauzimu ndipo afunikira kupitiriza kukula pansi pa chitsogozo ndi chithandizo chachikondi cha akulu ampingo. Amuna ameneŵa ayenera kukhala ophunzira akhama a Baibulo ndi zofalitsa zathu. Angasonyeze chifuno chawo mwa kugonjera kwa akulu oikidwa ndi mzimu, kutsanzira chikhulupiriro chawo, ndi kukhala ndi mikhalidwe yofunika mwa oyang’anira.—Aheb. 13:7, 17.
■ Kuyamba Utumiki wa Nthaŵi Yonse: Ntchito yaikulu ya mpingo ndiyo kulalikira uthenga wabwino. (Mat. 24:14) Limakhala dalitso chotani nanga pamene okangalika awonjezera changu chawo mwa kulembetsa upainiya! Nthaŵi zambiri zimenezi zimafuna kupanga masinthidwe m’moyo wawo. Pangafunikirenso masinthidwe ena kuti apitirize mu mbali ya utumiki wapadera umenewu. Koma aja amene amalimbikira mwaŵi umenewu m’malo mwa kusiya patapita chaka chimodzi kapena kuposapo chifukwa cha zovuta zakanthaŵi adzalandiradi madalitso ochuluka a Yehova. Akulu achikondi ndi ena okhwima angathandizire kwambiri chipambano cha apainiya, kuwalimbikitsa mwa mawu ndi zochitika. Ndi mzimu wabwino chotani nanga umene umasonyezedwa ndi achinyamata amene amayamba ntchito yaupainiya atangomaliza sukulu! Nawonso akulu amatero pamene alembetsa upainiya wokhazikika mathayo awo akuntchito atangochepa. Zimenezi zimapatsa Mkristu wodzipatulira chikhutiro chotani nanga pamene achita zinthu malinga ndi kufulumiza kwa Yehova ntchito yakututa!—Yes. 60:22.
■ Kuthandiza pa Ntchito Yomanga ndi Yosamalira Malo a Msonkhano: Kumadera ambiri a dziko kwamangidwa Nyumba Zaufumu zamakono mazana ambiri limodzi ndi Nyumba za Msonkhano. Chokondweretsa nchakuti, pafupifupi ntchito zonse zachitidwa ndi abale ndi alongo athu amene apereka mwaufulu nthaŵi yawo ndi maluso. (1 Mbiri 28:21) Antchito zikwi zambiri odzipereka mwaufulu amasamalira malo ameneŵa mwa kuchita ntchito iliyonse yofunika. (2 Mbiri 34:8) Kodi Nyumba yanu Yaufumu imapereka chitamando ndi ulemu kwa Yehova? Popeza kuti ntchito imeneyi ili mbali ina ya utumiki wopatulika, amene amathandiza amadzipereka iwo eni mwaufulu, osafunsira kulipiridwa kaamba ka utumiki wawo pantchitoyo, monga momwe sangafunsire kulipiridwa kuti alalikire kunyumba ndi nyumba, kukamba nkhani yapoyera mumpingo, kapena kuthandiza pantchito ya msonkhano wadera kapena wachigawo. Antchito odzifunira ameneŵa amachita mautumiki awo kwaulere pokonzekera ndi pomanga malo olambirira kuti apereke chitamando kwa Yehova. Amathandizira mofunitsitsa pa zinthu zonga kusaina zikalata zaboma, kusunga zolembedwa za maakaunti, kupeza kogula zinthu, ndi kuŵerengera unyinji wa milimo yofunikira. Atumiki a Yehova okhulupirika ameneŵa samalipiritsa zowonongeka zawo ndipo samafuna mwanjira iliyonse kupezapo phindu lakuthupi pa utumiki umene amachita, pakuti maluso awo onse ndi chuma chawo zili zopatulidwa kwa Yehova. Ntchito imeneyi imafuna antchito akhama ochita mautumiki awo “mochokera mumtima, monga kwa Ambuye.”—Akol. 3:23.
15 Pamenepa, kodi nchiyani chimene chimachititsa kudzipereka kwa anthu a Yehova kukhala kwapadera? Ndiwo mzimu wakupereka. Kupereka kwawo kooloŵa manja kumaphatikizapo zoposa ndalama kapena zinthu zakuthupi—iwo ‘amadzipereka eni ake [mwaufulu, NW ].’ (Sal. 110:3) Zimenezi ndizo tanthauzo lake la kudzipatulira kwathu kwa Yehova. Timafupidwa mwa njira yapadera. ‘Timadala kwambiri’ ndipo ‘timatuta mooloŵa manja’ chifukwa chakuti zimene timachita zimayamikiridwa ndi ena, amene amatipatsa nafenso. (Mac. 20:35; 2 Akor. 9:6; Luka 6:38) Wotifupa wopambana ali Atate wathu wakumwamba, Yehova, yemwe “akonda wopereka mokondwerera.” (2 Akor. 9:7) Iye adzatifupa ndi zochuluka, ndi madalitso osatha. (Mal. 3:10; Aroma 6:23) Chotero pamene mwaŵi ukufikani mu utumiki wa Yehova, kodi mudzadzipereka inu eni mwaufulu ndi kuyankha monga Yesaya kuti: “Ndine pano; munditumize ine”?—Yes. 6:8.