Kufika pa Misonkhano Nthaŵi Zonse—Chinthu Chofunika pa Kuchirimika Kwathu
1 Mtumwi Paulo anatisonkhezera kukhalabe “olama m’chikhulupiriro.” (Tito 1:9, 13) Pa misonkhano ya mpingo timakambitsirana malingaliro abwino ndipo timalangizidwa mmene tingadzivekere mokwanira zida zauzimu kotero kuti “[ti]khoze kuchirimika pokana machenjerero a Mdyerekezi.”—Aef. 6:11; Afil. 4:8.
2 Misonkhano Imapereka Zimene Timafuna: Kufika pa misonkhano ya mpingo nthaŵi zonse nkofunika pa kuchirimika kwathu. (1 Akor. 16:13) Mapemphero othokoza ndi kutamanda Mulungu amaperekedwa pa misonkhano, ndiponso kumupempha kuyang’anira mpingo ndi zosoŵa zake. (Afil. 4:6, 7) Kugwirizana nawo m’nyimbo kumatilimbikitsa ndi kutikhozetsa kusonyeza mmene timalingalilira pamene tikulambira Yehova. (Aef. 5:19, 20) Kuyanjana kwathu pamodzi pa Nyumba Yaufumu misonkhano isanayambe ndi pambuyo pake kumatilimbikitsa, kumatimangirira, ndipo kumatitsitsimula.—1 Ates. 5:11.
3 April wapitayo nkhani yapadera yakuti, “Mapeto a Chipembedzo Chonyenga Ayandikira,” inakhomereza mwamphamvu m’maganizo mwa okonda choonadi za kufunika kwa kufulumira kuchitapo kanthu kutuluka m’Babulo Wamkulu. (Chiv. 18:4) Kunali kotsitsimula chotani nanga kuphunzira nkhani zitatu za m’Nsanja ya Olonda m’June ndi m’July zonena za kuŵala kwa kuunika kumene kwaunikira njira ya olungama! (Miy. 4:18) Tangoganizirani zimene tikanaphonya ngati tikananyalanyaza kufika pa misonkhano imeneyo.
4 Pa Msonkhano wathu Wachigawo wakuti “Atamandi Achimwemwe,” panagogomezeredwa za kufunikira kwa maphunziro amene amakuza utumiki wathu. Monga momwe buku la Olinganizidwa Kutsiriza Uminisitala Wathu limasonyezera patsamba 72, Sukulu Yautumiki Wateokratiki ndiyo makonzedwe amaphunziro opita patsogolo a mpingo wonse. Sitiyenera konse kuphonya maphunziro ameneŵa.
5 Msonkhano Wathu Wautumiki umatikonzekeretsa kukhala ogwira mtima kwambiri mu utumiki. Zimenezi zinasonyezedwa ndi msonkhano wina umene tinalandiramo malangizo a kukhala ndi phande m’kugaŵira matrakiti a Uthenga wa Ufumu Na. 34 kwa anthu onse. Madalitso a Yehova pa ntchitoyi anali ochuluka, monga momwe tingaonere pa zotulukapo zake zabwino padziko lonse. (Yerekezerani ndi 2 Akorinto 9:6, 7.) Awo amene amafika pa misonkhano nthaŵi zonse analimbikitsidwa, ndipo anathandizira kupereka chichirikizo pa mkupitiwo.
6 Pa Phunziro Labuku Lampingo, chidziŵitso chathu cha chiphunzitso cha Baibulo chimakulitsidwa ndi zinthu zimene timaphunzira m’Mawu a Mulungu ndi chithandizo cha buku la Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona. Pamene zochitika zikupita patsogolo m’dziko, tifunikira kukulitsa ndi kuzamitsa luntha lathu la kumvetsa Mawu a Mulungu ndi kuwagwiritsira ntchito mokwanira bwino m’moyo wathu.
7 Chititsani Kufika pa Misonkhano Nthaŵi Zonse Kukhala Chinthu Choyamba: M’maiko ambiri mmene abale athu akupirira mayeso, amazindikirabe mmene kulili kofunikira kwa iwo kuti azisonkhana mlungu uliwonse. Mwachitsanzo, ku Burundi, Rwanda, Liberia, ndi ku Bosnia ndi Herzegovina, atsopano ambiri amafika pa misonkhano akumaposa chiŵerengero cha ofalitsa kuwirikiza kaŵiri kapena katatu. Mwa njira imeneyi Yehova amathandiza abalewo kukhalabe ochirimika mu mzimu umodzi.—Afil. 1:27; Aheb. 10:23-25.
8 Aliyense amene mwina wakhala akunyalanyaza kufika pa msonkhano nthaŵi zonse ayenera kutenga masitepe tsopano lino akuwongolera mkhalidwe umenewu. (Mlal. 4:9-12) Kuti tichirimike, tifunikira kulimbikitsana kogwirizana ndi aakulu msinkhu, kumene kumakhalapo pamene tisonkhana nthaŵi zonse.—Aroma 1:11.
Yapitirizidwa patsamba 3
Kufika (kuchokera patsamba 1)