Misonkhano Yautumiki ya November
Mlungu Woyambira November 6
Mph. 10: Zilengezo za pamalopo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu Waufumu.
Mph. 15: “Buku Latsopanolo Likusonyeza Chidziŵitso cha Mulungu.” Kukambitsirana kwa mafunso ndi mayankho. Limbikitsani onse kukhala odziŵa kwambiri za m’bukulo kuti aligwiritsire ntchito bwino m’munda.
Mph. 20: “‘Lemba Lililonse Lipindulitsa pa Chiphunzitso.’” Fotokozani mbali zina za New World Translation, mukumasonyeza chifukwa chake imaposa ena. Longosolani maubwino ake chifukwa cha kumasuliridwa kwake m’chinenero chamakono. (Onani buku la “All Scripture,” tsamba 328, ndime 4-6.) Sonyezani zitsanzo za maulaliki aŵiri.
Nyimbo Na. 2 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira November 13
Mph. 10: Zilengezo za pamalopo. Lipoti la maakaunti. Fotokozani makonzedwe a utumiki wakumunda kutha kwa mlungu uno.
Mph. 15: “Kufika pa Misonkhano Nthaŵi Zonse—Chinthu Chofunika pa Kuchirimika Kwathu.” Nkhani ndi kukambitsirana ndi omvetsera.
Mph. 20: “Mayendedwe Anu Ayenere Uthenga Wabwino.” Mafunso ndi mayankho. Nenani ndemanga zina zozikidwa pa Nsanja ya Olonda ya June 15, 1989, masamba 16-17, ndime 5-9.
Nyimbo Na. 23 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira November 20
Mph. 10: Zilengezo za pamalopo.
Mph. 15: Zosoŵa za pamalopo. (Kapena perekani nkhani yakuti “Kodi Mumakondwera ndi Phunziro Laumwini?” yozikidwa pa Nsanja ya Olonda ya June 15, 1994, masamba 8-11.)
Mph. 20: “Thandizani Ena Kudziŵa Phindu la Baibulo.” Mkulu akambitsirana ndi ofalitsa aŵiri kapena atatu chifukwa chake tiyenera kupanga maulendo obwereza ndi cholinga cha kuyambitsa maphunziro a Baibulo. Fotokozani ndiyeno sonyezani chitsanzo cha maulaliki osonyezedwawo a maulendo obwereza, powayesezera.
Nyimbo Na. 8 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira November 27
Mph. 10: Zilengezo za pamalopo.
Mph. 15: “Lingalirani za Kumwamba.” Mafunso ndi mayankho.
Mph. 20: Kugaŵira Buku Latsopano lakuti, Knowledge That Leads to Everlasting Life, m’December. Fotokozani mbali zokopa za bukulo—mitu ya nkhani yapadera kwambiri ndi zithunzithunzi zochititsa chidwi ndiponso mafotokozedwe ofeŵa, ukulu wake woloŵa m’thumba, ndi kugwiritsira ntchito kwake mafunso kwaluso. Tchulani mfundo zingapo zokambitsirana zimene zingakope anthu m’gawo lanu. Buku la Knowledge linalinganizidwa mwapadera kaamba ka kuchititsira maphunziro a Baibulo opita patsogolo, ndipo tiyenera kuyesayesa mwapadera kufikiranso amene tinawagaŵira, tili ndi cholinga cha kuyambitsa maphunziro a Baibulo. Itanani wofalitsa wokhoza bwino kuti adzachite chitsanzo cha ulaliki umodzi kapena maulaliki aŵiri achidule. Limbikitsani onse kugwiritsira ntchito bwino buku latsopano limeneli m’munda, kuyambira m’December.
Nyimbo Na. 78 ndi pemphero lomaliza.