Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu December: Knowledge That Leads to Everlasting Life. Yesetsani mwapadera kubwerera kumene munagaŵira mabukuwo, ndi cholinga choyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba. Mipingo imene ilibe buku latsopano limeneli ingagwiritsire ntchito buku la Munthu Wamkulu, buku la Nkhani za Baibulo, kapena buku la Kukhala ndi Moyo Kosatha. January: Gaŵirani buku la Moyo wa Banja pa mkupiti wapadera. Chogaŵira china chingakhale buku lililonse la masamba 192 limene mpingo ungakhale nalo m’sitoko. February: Buku la Moyo wa Banja pa mkupiti wapadera. Mipingo imene ilibe mtokoma wa mabuku ameneŵa ingagaŵire buku la Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona. March: Knowledge That Leads to Everlasting Life. CHIDZIŴITSO: Mipingo imene siinaodebe zinthu zamkupiti zotchulidwa pamwambazo iyenera kutero pa fomu yawo ya Literature Request (S-AB-14) ya mwezi ndi mwezi yotsatira.
◼ Mipingo iyenera kuyamba kuoda mabaundi voliyumu a 1995 a The Watchtower ndi Awake! pa oda yawo ya mabuku ya December. (Onani Mpambo wa Zofalitsa za Watch Tower, ndime 7, 8, 20.) Mabaundi voliyumu adzakhalako m’Chingelezi. Mabaundi voliyumu asanafike ndi kutumizidwa, adzasonyezedwa monga “Zoyembekezeredwa” pampambo wotumidwa ndi mitokoma. Mabaundi voliyumu ali zinthu za oda yapadera.
◼ Woyang’anira wotsogoza kapena winawake woikidwa ndi iye ayenera kuŵerengera maakaunti a mpingo pa December 1 kapena mwamsanga pambuyo pake. Lengezani ku mpingo mutachita zimenezi.
◼ Chikumbutso cha mu 1997 chidzakhalako pa Sande, March 23, dzuŵa litaloŵa. Chilengezo chapasadakhale chimenechi cha deti la phwando la Chikumbutso la 1997 chaperekedwa kuti abale abwereke kapena kupanga makonzedwe ofunikira a maholo ogwiritsira ntchito kumene mipingo ingapo imagwiritsira ntchito Nyumba ya Ufumu imodzi ndipo ifunikira kupeza malo ena.
◼ Zofalitsa Zomwe Zilipo:
Kalenda ya 1996—Chicheŵa, Chingelezi
Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku—1996—Chicheŵa, Chingelezi
Knowledge That Leads to Everlasting Life—Chingelezi