Misonkhano Yautumiki ya December
Mlungu Woyambira December 4
Mph. 10: Zilengezo zapamalopo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu Waufumu.
Mph. 15: “Tamandani Yehova Tsiku ndi Tsiku.” Mafunso ndi mayankho. Ŵerengani ndime zonse. Khalani ndi wofalitsa mmodzi kapena aŵiri kuti asimbe zokumana nazo zolimbikitsa zimene anapeza pochita ulaliki wamwamwaŵi.
Mph. 20: “Kugaŵira Buku la Knowledge That Leads to Everlasting Life.” Perekani chilimbikitso champhamvu cha kugaŵira buku latsopano, makamaka kwa aja amene anasonyezapo chidwi. Longosolani maulaliki osonyezedwawo, ndipo khalani ndi chitsanzo pa umodzi kapena aŵiri a ameneŵa.
Nyimbo Na. 224 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira December 11
Mph. 13: Zilengezo zapamalopo. Lipoti la maakaunti. Longosolani mwachidule zifukwa zimene tiyenera kulinganizira kutengamo mbali mokwanira ndi mwatanthauzo mu utumiki wakumunda. M’malo mothera ola limodzi lokha kapena kuposerapo pamene titulukira, bwanji osalinganiza kukhalamo kwa maola aŵiri kapena kuposapo ngati nkotheka? Kaŵirikaŵiri chipambano chimadalira pa kulinganiziratu maulendo obwereza ndi kulinganiza kugwira ntchito ndi ena amene akufuna kukhala mu utumiki kwa maola aŵiri kapena kuposapo.
Mph. 15: Zosoŵa zapamalopo. Kapena nkhani yozikidwa pankhani yakuti “Mfupo za Kulimbikira,” ya mu Nsanja ya Olonda ya August 1, 1995, masamba 25-9.
Mph. 17: “Konzekerani Misonkhano ya Mpingo ndi Kusangalala Nayo.” Nkhani ndi kukambitsirana. Itanani wofalitsa mmodzi kapena aŵiri kuti adzasimbe zimene amachita kuti asangalale ndi misonkhano ndi kupindula nayo kwambiri.
Nyimbo Na. 28 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira December 18
Mph. 10: Zilengezo zapamalopo. Perekani njira zoyankhira mwanzeru malonje a maholide. Lengezani makonzedwe apadera a ulaliki pa December 25.
Mph. 15: “Nthawi Zonse Pali Zochita Zochuluka.” Mafunso ndi mayankho. Konzani kufunsa kwa anthu aŵiri kapena atatu otanganitsidwa, monga mkulu, mkazi wokwatiwa, kapena mpainiya; apempheni afotokoze mmene amakwanitsira kuchita ntchito zonse ndi kukhalabe achimwemwe.
Mph. 20: “Bwererani kwa Aja Amene Anasonyeza Chidwi.” Longosolani maulaliki osonyezedwawo, ndipo khalani ndi zitsanzo ziŵiri zachidule. Limbikitsani onse kuchita maulendo obwereza ndi chonulirapo cha kuyambitsa maphunziro m’buku la Knowledge.
Nyimbo Na. 44 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira December 25
Mph. 5: Zilengezo zapamalopo. Ngati nthaŵi yanu ya misonkhano idzasintha kuyambira pa January 1, limbikitsani onse kuchirikiza zimenezi mwa kupanga kusintha kofunika. (Onani Utumiki Wathu Waufumu, wa December 1994, tsamba 2.) Lengezani makonzedwe apadera a ulaliki pa January 1.
Mph. 15: “Chititsani Kupita Kwanu Patsogolo Kuonekera.” Mafunso ndi mayankho.
Mph. 25: “Kuŵalitsa Kuunika Kwathu Mopitiriza.” Zikani mawu anu oyamba achidule pandime 1-5. Ndime 6-16 ziyenera kuchitidwa mwa mafunso ndi mayankho. Ŵerengani ndime 6-9, 15, ndi 16. Zikani mawu anu omaliza pandime 17-19. Yokambidwa ndi woyang’anira utumiki ngati nkotheka.
Nyimbo Na. 3 ndi pemphero lomaliza.