Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 12/95 tsamba 5-6
  • Kupenda Kolemba m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kupenda Kolemba m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
km 12/95 tsamba 5-6

Kupenda Kolemba m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki

Kupenda kolemba mabuku atatsekedwa pankhani zokambidwa m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki zogaŵiridwa kuyambira mlungu wa September 4 kufikira December 18, 1995. Gwiritsirani ntchito pepala lina kuti mulembepo mayankho ambiri othekera m’nthaŵi yoperekedwa.

[Tamverani: Mkati mwa kupendaku, gwiritsirani ntchito Baibulo lokha kuyankhira funso lililonse. Magwero a nkhani amene amaikidwa pambuyo pa mafunso ngoti mukadzifufuzire. Manambala a tsamba ndi ndime nthaŵi zonse sangasonyezedwe m’magwero onse a mu Nsanja ya Olonda.]

Yankhani kuti Zoona kapena Kunama m’ndemanga zotsatirazi:

1. “Mwana wamwamuna” wotchulidwa pa Yesaya 66:7 amaimira kubadwa kwa mtundu wauzimu wa Akristu odzozedwa mu 1919, osati kubadwa kwa Ufumu Waumesiya mu 1914. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w89-CN 9/1 tsa. 18.]

2. Yesaya 38:5 amatithandiza kumvetsetsa kuti mapembedzero oona mtima angasonkhezere Yehova kuchita chinthu chimene sakanachita. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w95-CN 4/1 tsa. 15.]

3. Munthu wa pa dziko lapansi wosanunkha kanthu angachititse Mlengi wa chilengedwe chonse kupwetekedwa mtima kapena kusangalala. (Yes. 63:10) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w93-CN 6/15 tsa. 15.]

4. Yeremiya 1:5 amachirikiza zimene Baibulo limasonyeza kuti moyo umayambira pamene mimba ikhala. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w89-CN 6/15 tsa. 29.]

5. Yesaya 53:5, 12 ananeneratu kuti Yesu Kristu adzafa monga nsembe ya dipo kukwirira machimo a ena. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w92-CN 10/1 tsa. 14.]

6. Yesaya 48:17 kwenikweni amatiuza kuti tigwiritsire ntchito Mawu a Mulungu m’moyo wathu ndi kudzionera tokha kuti zitsogozo zopezeka mmenemo zimagwiradi ntchito. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w95-CN 3/1 tsa. 12.]

7. Ngakhale kuti Mboni za Yehova sizimatenga mbali mpang’ono pomwe m’machitachita andale, izo sizimaletsa zimene ena amachita monga kuloŵa m’chipani cha ndale, kuima pachisankho kuti avoteredwe paudindo m’boma, kapena kuvota pachisankho. [uw-CN tsa. 166 ndime 12]

8. Atumiki a Mulungu okhulupirika amene anakhalako Kristu asanafike sanadziŵe kalikonse za dziko latsopano limene tikuliyembekezera. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w95-CN 2/15 tsa. 11.]

9. Koresi anakhala “wodzozedwa” wa Yehova ngakhale kuti palibe umboni wosonyeza kuti mafuta enieni anatsanuliridwa pa iye. (Yes. 45:1) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w92-CN 11/15 tsa. 30.]

10. Kuti atumikire Mulungu ndi kudzipereka konse, Akristu ayenera kudziŵa tsiku ndi ola pamene Yehova adzawononga dongosolo la Satana la dziko lapansi. [uw-CN tsa. 176 ndime 2]

Yankhani mafunso otsatirawa:

11. Kodi ndi liti pamene Mkristu ayenera kulankhula ndi dokotala wake za chosankha chake cha kusala mwazi? [uw-CN tsa. 158 ndime 9]

12. Kodi Yesu sanali mbali ya dziko mwa njira yotani? [uw-CN tsa. 161 ndime 2]

13. Kodi kulankhula Mawu a Mulungu molimba mtima sikumatanthauzanji? [uw-CN tsa. 175 ndime 13]

14. Ngati timakondadi uthenga wabwino, kodi ndi thayo lotani limene tili nalo? [uw-CN tsa. 169 ndime 2]

15. Pa mitundu yonse ya pa dziko lapansi, kodi ndi uti umene uli “mtundu wolungama, umene uchita zoonadi” kulinga kwa Mulungu, ndipo ndi ayani omwe akuwonjezedwa ku mtundu umenewo? (Yes. 26:2, 15) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w95-CN 1/1 mas. 10, 11.]

16. Malinga ndi Yesaya 32:1, 2, kodi ntchito yaikulu ya akulu nchiyani? [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu: onani w93-CN 4/1 tsa. 30.]

17. Kodi ndi chipatso choonekera bwino chotani chimene chiphunzitso chaumulungu chatulutsa pakati pa Mboni za Yehova kuzungulira dziko lonse? (Yes. 54:13) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w94-CN 3/1 tsa. 17.]

18. Kodi ndi m’mabuku ndi machaputala ati mmene Mauthenga Abwino atatu amalongosola za chizindikiro chachiungwe chosonyeza “mathedwe a nthaŵi ya pansi pano”? [uw-CN tsa. 178 ndime 5]

19. Kodi nchifukwa ninji m’mbiri yolembedwa ya Sanakeribu, iye sanakhoze kudzitama za kugonjetsa kwake likulu la Yuda, Yerusalemu, mmene anadzitamira za kugonjetsa kwake mzinda wa Yuda wa linga wa Lakisi? (Yes. 37:36) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w93-CN 6/1 tsa. 6.]

20. Kodi “ching’ona” chotchulidwa pa Yesaya 27:1 chimachitira chithunzi yani ndi chiyani? [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w86 8/15 tsa. 31.]

Perekani liwu kapena mawu ofunika kutsiriza ndemanga zotsatirazi:

21. Pamene Mkristu alembedwa kuti asungidwe m’chipatala, ayenera ․․․․․․․ pempho lakuti mwazi suyenera kugwiritsiridwa ntchito, ndipo ayenera ․․․․․․․ za nkhaniyo kwa dokotala amene adzasamalira matenda ake. [uw-CN tsa. 158 ndime 9]

22. Njira ziŵiri zimene timasonyezera chidaliro chathu pa Yehova ndizo mwa kupezeka ․․․․․․․ mokhazikika ndi mwa kumapita kwa Iye nthaŵi zonse ․․․․․․․. [uw-CN mas. 170-1 ndime 5-7]

23. Pamene misonkhano yadera ilinganizidwa m’dera lililonse, ․․․․․․․ ndiye ali ndi thayo la kayendetsedwe ka msonkhanowo. Amathandizana kwambiri ndi ․․․․․․․. [om-CN tsa. 50 ndime 1]

24. Makonzedwe otchulidwa pa Aefeso 1:9, 10 amasumika pa ․․․․․․․, ndipo kupyolera mwa iye anthu amaloŵa mumkhalidwe ․․․․․․․ pamaso pa Mulungu, ena ndi chiyembekezo chokakhala ․․․․․․․ , ena pa ․․․․․․․. [uw-CN tsa. 186 ndime 6]

25. “Ana a Mulungu” otchulidwa pa Aroma 8:19-21 ali ana odzozedwa ndi mzimu amene alandira mphoto ․․․․․․․ , ndipo adzavumbulidwa pamene anthu pa ․․․․․․․ aona umboni wakuti iwo ayamba kuchitapo kanthu, akumathandizana ndi Kristu ․․․․․․․ dongosolo la zinthu loipali. [uw-CN tsa. 188 ndime 11]

Sankhani yankho lolondola m’ndemanga zotsatirazi:

26. Akristu oyambirira ananyozedwa kuti anali akuda fuko la anthu chifukwa chakuti (sankalankhula kwa osakhulupirira; sanalambire mafano; anapeŵa zosangulutsa zachiwawa ndi zachisembwere). [uw-CN tsa. 163 ndime 7]

27. M’fanizo la Yesu pa Mateyu 13:36-43, tirigu amaimira (anthu okhulupirika akale; khamu lalikulu; Akristu odzozedwa), ndipo namsongole amaimira (osakhulupirira onse; Akristu achiphamaso; Alembi ndi Afarisi). [uw-CN tsa. 179 ndime 7]

28. Pambuyo pakuti olamulira andale awononga chipembedzo chonyenga, mwamwano adzatembenukira kwa (dongosolo la malonda; United Nations; awo ochirikiza ulamuliro wa Yehova). [uw-CN tsa. 182 ndime 13]

29. Mu 1914 panali anthu pafupifupi (1,100; 5,100; 10,100) amene anali kulalikira mokangalika. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w94-CN 9/1 tsa. 16.]

30. Amene amathandiza Komiti ya Nthambi pa mavuto kapena mafunso amene amayang’anizana nawo pa ntchito ya kulalikira ndi kupanga ophunzira ndi ya kuyendetsa nthambi ndi woyang’anira (dera; chigawo; woyendera nthambi). [om-CN tsa. 53 ndime 3 ndi tsa. 54 ndime 1]

Gwirizanitsani malemba otsatirawa ndi ndemanga zondandalikidwa pansipa:

Lev. 17:11, 12; Yes. 43:10; Yer. 7:31; Yoh. 8:41, 44, 47; Mac. 4:13

31. Kukhala ndi maphunziro ochepa akusukulu sikumalepheretsa munthu kukhala mlaliki wopanda mantha wa uthenga wabwino. [uw-CN tsa. 172 ndime 8]

32. Njira yokha ya Malemba imene mwazi unagwiritsiridwa ntchito imasonyeza kupatulika kwake ndi kugogomezera mtengo wa nsembe ya Kristu. [uw-CN tsa. 159 ndime 11]

33. Machitidwe a munthu ndi mzimu umene amasonyeza zimavumbula moonekera bwino amene ali atate wake wauzimu kuposa mmene mawu ake amavumbulira. [uw-CN tsa. 185 ndime 5]

34. Yehova alibe womtsogolera kukhalako; kunalibe mulungu wina iye asanakhaleko, ndipo sikudzakhala aliyense pambuye pake chifukwa chakuti ali wamuyaya, Mfumu Yam’mwambamwamba. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w92-CN 1/15 tsa. 22.]

35. Achikulire ambiri lerolino sangalingalire nkomwe za kupereka ana awo nsembe ku mafano, komabe mamiliyoni osaŵerengeka a makanda akuphedwa dala mwa kutaya mimba, ndipo mamiliyoni a achichepere aperekedwa pa guŵa lansembe la nkhondo. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w88-CN 1/15 tsa. 31.]

S-97-CN Mal, Moz & Zam #287b 12/95

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena