Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 1/96 tsamba 3
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
km 1/96 tsamba 3

Zilengezo

◼ Mabuku ogaŵira mu January: Gaŵirani buku la Moyo wa Banja pa mkupiti wapadera. Chogaŵira china chingakhale buku lililonse la masamba 192 limene mpingo ungakhale nalo m’stoko. February: Buku la Moyo wa Banja pa mkupiti wapadera. Mipingo imene ilibe mtokoma wa mabuku ameneŵa ingagaŵire buku la Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona. March: Knowledge That Leads to Everlasting Life. April: Sabusikripishoni ya Nsanja ya Olonda. CHIDZIŴITSO: Mipingo imene siinaodebe zinthu zamkupiti zotchulidwa pamwambazo iyenera kutero pa fomu yawo ya Literature Order (S-AB-14) ya mwezi ndi mwezi yotsatira.

◼ Mipingo iyenera kupanga makonzedwe oyenera a kuchita Chikumbutso chaka chino pa Lachiŵiri, April 2, dzuŵa litaloŵa. Ngakhale kuti ndi bwino kuti mpingo uliwonse uchite Chikumbutso pa uwo wokha, nthaŵi zina zimenezi sizimatheka. Kumene mipingo yambiri imagwiritsira ntchito Nyumba ya Ufumu imodzi, mwina mpingo umodzi kapena ingapo ingagwiritsire ntchito malo ena madzulowo. Chikumbutso sichiyenera kuyamba mochedwa kwambiri kwakuti okondwerera chatsopano nkulephera kupeza nthaŵi yofikapo. Ndiponso, programu yake siyenera kukhala yopanikiza kwambiri kwakuti nkulephera kupeza nthaŵi ya kupatsa moni alendo kuchiyambi ndi kumapeto kwa chochitikacho, kupanga makonzedwe akupitiriza kupereka chithandizo chauzimu kwa ena, kapena kulimbikitsana kwa onse. Pambuyo popenda zonse zoloŵetsedwamo, akulu ayenera kupanga makonzedwe amene adzathandiza bwino lomwe awo opezeka pa Chikumbutso kupindula kwambiri ndi chochitikacho.

◼ Nkhani yapadera ya nyengo ya Chikumbutso ya 1996 idzakambidwa pa Sande, April 21. Mutu wake udzakhala wakuti “Kukhala Opanda Banga Pakati pa Mbadwo Wokhotakhota.” Autilaini yake idzatumizidwa. Mipingo imene idzakhala ndi woyang’anira dera, msonkhano wadera, kapena msonkhano wa tsiku lapadera kutha kwa mlungu umenewo idzakhala ndi nkhani yapaderayo mlungu wotsatira. Palibe mpingo uliwonse umene yenera kupereka nkhani yapaderayo April 21 asanafike.

◼ Kuyambira mu February, ndipo mosapyola pa March 3, nkhani yapoyera yatsopano ya oyang’anira madera idzakhala yakuti “Mpingo Wokhulupirika Pansi pa Utsogoleri wa Kristu.”

◼ Chopereka cha kabuku la Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku chidzakhala chofanana kwa apainiya ndi ofalitsa omwe. Chonde sinthani zimenezi moyenera pa mpambo wa mitengo.

◼ Mipingo yonse imene ili ndi matrakiti a Uthenga wa Ufumu Na. 34 m’sitoko iyenera kuwagaŵira mu utumiki wawo wakumunda wanthaŵi zonse monga momwe amagaŵirira matrakiti Na. 13-16 ndi 19-22. Tidakali ndi ena m’sitoko kuno ku Nthambi ndipo mukhoza kuwaoda monga momwe mumaodera matrakiti ena. Zinenero za matrikiti omwe ali m’sitokowa ndizo: Chicheŵa, Chingelezi ndi Chitumbuka.

◼ Zofalitsa Zomwe Zilipo:

“All Scripture is Inspired of God and Beneficial”—Chingelezi

Revelation—Its Grand Climax At Hand—Chingelezi

Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona—Chicheŵa

◼ Zofalitsa Zomwe Sizidzakhalakonso m’Sitoko:

Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi (laling’ono ndi lalikulu)—m’zinenero zonse.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena