Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 1/96 tsamba 3
  • Lankhulani Molimba Mtima

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Lankhulani Molimba Mtima
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Nkhani Yofanana
  • ‘Lankhulani Mawu a Mulungu Molimba Mtima’
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Tsanzirani Yesu mwa Kulalikira Molimba Mtima
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Lalikirani Uthenga Wabwino Paliponse
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Pitirizani Kulankhula Mawu a Mulungu Molimbika Mtima
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
km 1/96 tsamba 3

Lankhulani Molimba Mtima

1 M’zaka zaposachedwapa ofalitsa a m’madera ena akupeza kulankhula ndi anthu panyumba zawo kukhala kovuta mowonjezereka. Ambiri amasimba kuti theka la anthu a m’dera lawo samapezeka pamene afikira nyumba ndi nyumba. Chotero, nthaŵi yochuluka imene amawononga imakhala yosapindulitsa.

2 Zaka zapitazo anthu ambiri anali kupezeka panyumba patsiku la Sande, limene ambiri analiona kukhala tsiku la kupuma. Miyambo yasintha. Lerolino kuli kofala kwa anthu kugwira ntchito zolembedwa, kupezera banja zofunika monga ngati kukagula zinthu, kapena kusanguluka, kumenenso kumawachititsa kusapezeka panyumba. Chotero ngakhale pamasiku a Sande, kulankhula ndi anthu kunyumba ndi nyumba kwakhala vuto.

3 Pamene anthu sali panyumba, mwachionekere zimatanthauza kuti amakhala ali kwina. Popeza kuti chonulirapo chathu chili cha kulankhula ndi anthu, bwanji osalankhula ndi aja amene timakumana nawo—pakhwalala, pamsika, kapena kuntchito. Paulo anali ndi chizoloŵezi cha kufikira “iwo amene anakomana nawo,” kuti awachitire umboni. (Mac. 17:17) Zimenezi zinalidi mtundu wina wochitira umboni wopindulitsa panthaŵiyo, ndipo udakali mtundu wopindulitsa wochitira umboni m’tsiku lathu.

4 Pamene tipita kunyumba ndi nyumba, kaŵirikaŵiri timaona anthu akuwongola miyendo kapena akuyembekezera munthu wina. Patsiku la kucha bwino, iwo angakhale pa mabenchi a m’paki kapena akumakonza kapena kutsuka galimoto lawo. Kumwetulira kwaubwenzi ndi kupereka moni kwaubwenzi zingangokhala zinthu zimene tifunikira kuchita kuti tiyambitse kukambitsirana. Ngati iwo amakhala pafupi ndi kwathu, tingathe kutchula kuti mwina tinangophonyana nawo panyumba pawo ndi kuti tsopano tili okondwa kuti tapeza mpata umenewu wa kulankhula nawo. Mwa kuyamba kusonyeza kulimba mtima pang’ono, ambiri akhala ndi zokumana nazo zofupa.

5 Kulimba Mtima Kumatulutsa Zipatso: Mbale wina anasimba kuti amafikira anthu amene ali chilili, omayembekezera basi, amene akuwongola miyendo, kapena amene akhala m’galimoto lawo. Pokhala akumwetulira ndi kulankhula mwansangala, amawafikira monga mnansi waubwenzi amene akungocheza ndi anthu. Mwa njira imeneyi iye sanangogaŵira chabe mabuku ochuluka komanso wayambitsa maphunziro a Baibulo angapo.

6 Mbale wina ndi mkazi wake anali m’ntchito yakukhomo ndi khomo pamene anakumana ndi mkazi wina amenenso anali kuyenda atanyamula thumba lalikulu la zogulagula za kugolosale. Anayamba kukambitsirana naye, akumamuyamikira chifukwa cha khama lake posamalira zosoŵa za banja lake. “Koma kodi ndani,” iwo anafunsa motero, “amene angathe kugaŵira zosoŵa za anthu?” Zimenezo zinadzutsa chidwi cha mkaziyo. Kukambitsirana kwachiduleko kunamchititsa kuwaitanira kunyumba kwake, kumene phunziro la Baibulo linayambidwa.

7 Chotero nthaŵi ina pamene muchitira umboni kukhomo ndi khomo, kaya pakhale pa Sande kapena patsiku lina lililonse lamlungu, ndipo mupeza kuti anthu sali panyumba, bwanji osalimbika mtima pang’ono ndi kulankhula kwa anthu amene mukukumana nawo—pakhwalala kapena kwina kulikonse? (1 Ates. 2:2) Utumiki wanu ungakhale wopindulitsa kwambiri, ndipo mudzapeza chimwemwe chachikulu kwambiri mu utumiki wanu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena