Pitirizani Kulankhula Mawu a Mulungu Molimbika Mtima
1 Monga atumiki achikristu, tikudziwa kuti si anthu onse amene amamvetsera ulaliki wathu. (Mat. 10:14) Komabe, sitifunikira kulola kusamvetsera kwa anthu ena kutilepheretsa kulalikira uthenga wabwino. (Miy. 29:25) Kodi chingatithandize n’chiyani kuti tizilankhula Mawu a Mulungu molimbika mtima?
2 Mtumwi Paulo anayamikira “mapambanidwe a chizindikiritso cha Kristu Yesu.” Zimenezi zinamuthandiza kulankhula “mosakayika konse.” (Afil. 3:8; 1 Ates. 1:5, Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chichewa Chamakono) Ngakhale kuti ena ankaona uthenga umene Paulo ankaulalikira monga wopanda phindu ndi wopusa, iye ankauona monga “mphamvu ya Mulungu yakupulumutsa munthu aliyense wakukhulupira.” (Aroma 1:16) Choncho, ngakhale pamene ankakumana ndi otsutsa, anapitirizabe, “nanenetsa zolimba mtima mwa Ambuye.”—Mac. 14:1-7; 20:18-21, 24.
3 Gwero la Mphamvu Zathu: Paulo sanachitire umboni molimbika mtima chifukwa cha mphamvu zake ayi. Polankhula za iye mwini ndi Sila, Paulo anati: ‘Tingakhale tidamva zowawa kale, ndipo anatichitira chipongwe . . . ku Filipi, tinalimbika pakamwa mwa Mulungu wathu kulankhula ndi inu Uthenga Wabwino wa Mulungu m’kutsutsana kwambiri.’ (1 Ates. 2:2; Mac. 16:12, 37) Ndiponso, ali m’ndende ku Roma, anapempha anthu ena kuti amupempherere kuti apitirize ‘kulankhula molimbika, monga anayenera kulankhula,’ polalikira uthenga wabwino. (Aef. 6:18-20) Mwa kudalira Yehova m’malo modzidalira yekha, Paulo anapitirizabe kulankhula Mawu a Mulungu molimbika mtima.—2 Akor. 4:7; Afil. 4:13.
4 Zimenezi n’zoonanso masiku ano. Mbale wina amene zinkamuvuta kwambiri kuuza anzake kuntchito kuti iyeyo ndi wa Mboni za Yehova ndi kuwalalikira anapemphera kuti asinthe maganizo amenewa ndipo atatero, anayamba kulalikira. Poyamba, mnzake wina kuntchitoko anakana kumvetsera. Koma atamva zoti akufa adzauka, anayamba kuphunzira Baibulo. Kuchokera pamenepo, mbaleyu anagwiritsa ntchito mpata uliwonse kuchitira umboni. Atakalowa ntchito kwina, anathandiza anthu ogwira nawo ntchito okwana 34 kubatizidwa pa zaka 14. Tili ndi chikhulupiriro choti Yehova angatilimbitsenso mofanana ndi mbaleyu kuti ‘tilankhule mawu ake ndi kulimbika mtima konse.’—Mac. 4:29.