Kodi Mumalalikira Molimba Mtima?
1 Petro ndi Yohane anapitiriza kulalikira uthenga wa Ufumu molimba mtima ngakhale kuti anagwidwa ndiponso anaopsezedwa ndi otsutsa. (Mac. 4:17, 21, 31) Kodi kulalikira molimba mtima kumatanthauzanji kwa ife lerolino?
2 Kuchitira Umboni Molimba Mtima: Mawu ofanana ndi mawu akuti “kulimba mtima” ndi “kupanda mantha,” kutanthauza kuti “kusaopa kanthu, kulimba, ndi kupirira.” Kwa Akristu oona, kulalikira molimba mtima kumatanthauza kusaopa kulankhula ndi ena za uthenga wabwino nthaŵi zonse mpata ukapezeka. (Mac. 4:20; 1 Pet. 3:15) Kumatanthauza kuti sitichita manyanzi ndi uthenga wabwino. (Sal. 119:46; Aroma 1:16; 2 Tim. 1:8) Chotero, kulimba mtima ndi mkhalidwe wofunika kuti tikwaniritse ntchito yathu yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu m’nthaŵi ya mapeto ino. Kumatisonkhezera kuuza anthu uthenga wabwino kulikonse kumene angapezeke.—Mac. 4:29; 1 Akor. 9:23.
3 Kulimba Mtima Kusukulu: Kodi mantha ndi manyazi zimakulepheretsani kulalikira kwa anzanu akusukulu? Nthaŵi zina zimavuta; ndipotu lingakhale vuto lalikulu. Komabe, Yehova adzakulimbikitsani ngati mupemphera kuti alimbitse mtima wanu kuti muthe kulalikira ena. (Sal. 138:3) Kulimba mtima kudzakuthandizani kudzidziŵikitsa kuti ndinu wa Mboni za Yehova ndiponso kupirira ponyozedwa. Ngati mulalikira kusukulu mudzapulumutsa amene amakumvetserani.—1 Tim. 4:16.
4 Kulimba Mtima Kuntchito: Kodi kuntchito mumadziŵika kuti ndinu wa Mboni za Yehova? Njira yokha imene anzanu akuntchito angamvere uthenga wabwino ingakhale kuwalalikira inuyo. Kulimba kwanu mtima kudzakuthandizaninso kupempha nthaŵi kuntchito yopita ku misonkhano yanu ya mpingo ndi misonkhano ikuluikulu.
5 Kulimba Mtima Poyesedwa: N’kofunika kukhala wolimba mtima pachitsutso. (1 Ates. 2:1, 2) Kumatithandiza kugwiritsitsa chikhulupiriro chathu pamene tikuopsezedwa, kunyozedwa, kapena pamene tikuzunzidwa kumene. (Afil. 1:27, 28) Kumatilimbitsa kuima nji pokakamizidwa kuswa miyezo ya Mulungu wathu, Yehova. Kumatilimbikitsa kusungabe mtendere pamene ena ayambitsa mikangano.—Aroma 12:18.
6 Kaya aliyense wa ife amakumana ndi mavuto amtundu wanji, tipitirizetu kulalikira uthenga wabwino molimba mtima.—Aef. 6:18-20.