Opani Yehova Tsiku Lonse
1 “Kumuopa Yehova ndiko chiyambi cha nzeru.” (Sal. 111:10) Kumatilimbikitsa kuchita ntchito zabwino ndipo kumatithandiza kupatuka pa choipa. (Miy. 16:6) Kuopa uku ndi kum’patsa Mlengi wathu ulemu wakuya, kumene kumatisonkhezera kupeŵa kusam’kondweretsa ndi kusamumvera. Ndi mkhalidwe umene tikufunika kuukulitsa ndi kuusonyeza tsiku lonse.—Miy. 8:13.
2 Tsiku ndi tsiku, mzimu wa dziko la Satana umatisonkhezera kwambiri kuti titsatire njira zake zoipa. (Aef. 6:11, 12) Thupi lathu lopanda ungwiro n’lochimwa ndipo mwachibadwa limafuna kuchita choipa. (Agal. 5:17) Pachifukwa chimenechi, kuti titsatire malamulo a Yehova, kuti tikhale achimwemwe, ndi kuti tipeze moyo, tiyenera kumuopa tsiku lonse.—Deut. 10:12, 13.
3 Pa Ahebri 10:24, 25, timalangizidwa kusonkhana pamodzi kuti tilimbikitsane “koposa” m’nthaŵi zimene tikukhalamo zino. N’kofunika kupezeka pamisonkhano nthaŵi zonse ngati tikufuna kupirira masiku otsiriza ano. Kuopa kusakondweretsa Mulungu kumatisonkhezera kupezeka pamisonkhano komanso kuyamikira kwambiri cholinga chake. Anthu amene amaopa Mulungu, kupezeka pamisonkhano yachikristu amakuona kukhala mwayi wopatulika.
4 Njira ina imene timasonyezera kuopa kwathu Mulungu ndiyo kumvera lamulo lolalikira uthenga wabwino wa Ufumu. (Mat. 28:19, 20; Mac. 10:42) Cholinga chenicheni cha ntchito yathu yolalikira ndi kuthandiza ena kuopa Yehova ndi kugonjera chifuno chake. Timachita zimenezi mwa kupanga maulendo obwereza, poyesetsa kuyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba, ndiponso kuphunzitsa ena malamulo onse a Mulungu. Mwanjira imeneyi timasonyeza kuti timaopa Yehova ndi kuti timakonda anansi athu.—Mat. 22:37-39.
5 Anthu amene saopa Mulungu sakhala ndi mtima woyamikira zinthu zauzimu, ndipo amatsatira mphweya wakupha wa dzikoli, kapena malingaliro ake. (Aef. 2:2) Chosankha chathu chenicheni chikhaletu ‘kutumikira Mulungu mom’kondweretsa, ndi kum’chitira ulemu ndi mantha.’ (Aheb. 12:28) Tikatero tidzapeza madalitso amene anthu oopa Yehova tsiku lonse amapeza.