Bokosi la Mafunso
◼ Kodi nkoyenera kwa munthu kupereka ndalama pamene ena amnyamula pagalimoto lawo?
Ena a ife tili m’mikhalidwe imene imatipangitsa kudalira pa ena kuti atithandize kufika pamisonkhano mokhazikika ndi kukhala ndi phande mu utumiki wakumunda. Abale ndi alongo ambiri amayesa kuthandiza mokoma mtima ndipo mwachikondi akumagwiritsira ntchito nthaŵi yawo, galimoto, ndi chuma china kuti atiyendetse ulendo. Ngakhale kuti angafunikire kukonzekera mofulumirirapo kuposa mmene akanachitira ndipo amachedwetsedwa kubwerera kwawo, amanyamula ena pagalimoto mwaufulu.
Monga momwe zilili ndi mbali zonse za utumiki wathu wachikristu, lamulo lopezeka pa Agalatiya 6:5 limakhudza mbali imeneyi: “Yense adzasenza katundu wake wa iye mwini.” Chifukwa chake, ngati wina amatinyamula pagalimoto nthaŵi zonse, tiyenera kusonyeza chiyamikiro chathu osati ndi mawu okha komanso, ngati tingathe, ndi ndalama zoyenera kuthandizira kugulira zofunika zoloŵetsedwamo.—Mat. 7:12; 1 Akor. 10:24.
Ngakhale ngati munthu amene akugwiritsira ntchito galimoto yakeyo sapempha thandizo la ndalama ndipo achita ngati salifuna, ndalama zothandizira zoperekedwa moona mtima amaziyamikira nthaŵi zonse. Woyendetsa galimoto angakane kulandira chilichonse; ndipo, ndithudi, zimenezo ziyenera kukhala chosankha chake. Koma kuli koyenera kuti inuyo mupereke ndalamazo. Ngati muli wosakhoza kupereka chilichonse panthaŵiyo, mungakumbukirebe zimenezo; mwina mukhoza kudzapereka ndalama zowonjezereka panthaŵi ina pamene muyenda pagalimoto lake.—Luka 6:38.
Chili chikondi chachikulu cha aja amene ali ndi galimoto kunyamula ena amene sakanatha kufika kumisonkhano kapena kukhala ndi phande mu utumiki wakumunda. (Miy. 3:27) Panthaŵi imodzimodziyo, chili chikondi cha aja amene amapindula ndi kukoma mtima kotero kusonyeza chiyamikiro chawo mwa kuchirikiza ndi ndalama mogwirizana ndi mikhalidwe yawo.—Akol. 3:15.