Kodi Mungathandize?
1 Mtumwi Paulo analimbikitsa anthu a mu mpingo kuti ‘asamalane wina ndi mnzake.’ (1 Akor. 12:25) Choncho, tiyenera kusonyeza chidwi mwa ena ndi kukhala ofunitsitsa kupereka thandizo mwachikondi pamene kuli kofunika. Mwachitsanzo, alongo ena achikristu pakati pathu akulera okha ana m’choonadi. Alongo amenewa ali ndi udindo wonse wopereka kwa ana awo maphunziro auzimu. Ndithudi ndi ofunika chilimbikitso chathu chachikondi ndi kuwathandiza “malinga ndi zosoŵa zawo.” (Aroma 12:13a, NW) Kodi mungawathandize?
2 Njira Zimene Mungathandizire: Kuthandiza mayi kutenga ana ake kupita kumisonkhano, ngakhale kuwathandiza ndi ndalama kuti athe kufika pamisonkhano ikuluikulu, kungakhale kwabwino kwambiri. Kuthandiza mayi kusamalira mwana wawo wamng’ono pamisonkhano kungathandize kuti apindule kwambiri ndi pologalamu. Mofananamo, kumuthandiza pamene watenga ana mu utumiki wakumunda kungamupangitse kukhala wopepukidwako. Kusonyeza chidwi chenicheni mwa ana—kucheza nawo—kungathandize kwambiri kulimbikitsa achinyamata athu m’njira yabwino. Nthaŵi zina kuitana banja la kholo limodzi kudzakhala nawo pa phunziro lanu la banja kungapereke chilimbikitso chotsitsimula mwauzimu.
3 Khalani Wanzeru: Tiyenera kusamala kuti tisakakamire kuthandiza amene sakufuna kuthandizidwa. Kapena kuloŵerera mu nkhani zaumwini pamene tikupereka thandizo. N’zoona, alongo ndi anthu okwatira ndiwo angapereke bwino thandizo kwa mlongo amene akufunikira thandizo.
4 Akristu onse akulimbikitsidwa ‘kucherezana’ wina ndi mnzake. (Aroma 12:13b) Kuthandiza abale ndi alongo athu auzimu ndi imodzi mwa njira zambiri zimene tingasonyezere chikondi chonga cha Kristu chimene tili nacho pakati pathu.—Yoh. 13:35.