Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu April ndi May: Sabusikripishoni ya Nsanja ya Olonda. June: Knowledge That Leads to Everlasting Life. July ndi August: Lililonse la mabrosha otsatirawa amasamba 32: Boma Limene Lidzabweretsa Paradaiso, Kodi Chifuno cha Moyo Nchiyani—Kodi Mungachipeze Motani?, Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu?, Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira, Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha!, “Tawonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano.” Pamene kuli koyenera, mabrosha monga Mizimu ya Akufa—Kodi Ingakuthandizeni Kapena Kukuvulazani? Kodi Iyo Ilikodi?, Our Problems—Who Will Help Us Solve Them?, ndi Will There Ever Be a World Without War? angagaŵiridwe.
◼ Kumene kuli kotheka akulu ayenera kupanga makonzedwe akuti mpingo uzithera nthaŵi yochuluka mu umboni wa madzulo.
◼ Kwa oyang’anira otsogoza: Tikupemphani kutumiza ku Sosaite zokumana nazo zilizonse zapadera zimene mpingo wakhala nazo chaka chino, kuphatikizapo zokumana nazo za utumiki waupainiya wothandiza ndi tsiku lapadera la magazini m’April 1996. Tikufuna kusankha zabwino koposa kuchokera m’munda wathu kaamba ka lipoti la chaka. Chonde tumizani zimenezi pofika mwezi wa maŵa, May 1996. Chonde kumbukirani kutipatsa chidziŵitso chakuti kaya munthu wopereka zokumana nazozo ali wofalitsa wokhazikika ndipo ali ndi kaimidwe kabwino mumpingo, dzina lake ndi dzina la mpingo umene akugwirizana nawo. Madeti a zokumana nazo, maina a malo ndi anthu otchulidwa m’zokumana nazo, ndiponso dzina la woyang’anira wotsogoza liyenera kuperekedwa lonse.
◼ Tikusintha njira yopatsira makadi ena a Pioneer Service Identification. Kuyambira tsopano, makadi ena a apainiya osamuka, kusintha maina awo, otaya makadi awo, kapena opempha kusintha gawo adzaperekedwa ndi Sosaite. Makadi alionse osalembedwapo kanthu amene mlembi angakhale nawo m’faelo ayenera kuwataya. Kusintha maina ndi magawo kudzasamaliridwa monga mwa masiku onse, mlembi akumalemba chidziŵitso chofunikira kuseri kwa Lipoti la Mpingo (S-1) la mweziwo. Pambuyo pake, Sosaite idzatumiza kumpingowo makadi atsopano a apainiya. Masinthidwe alionse ayenera kutumizidwa ku Sosaite mwamsanga kuti mafaelo athu akhale olondola ndi atsopano. Ndiponso, pamene mpainiya wasiya utumikiwo kapena wafafanizidwa, kope la fomu ya S-206 liyenera kudzazidwa ndi kutumizidwa ku Sosaite mwamsanga.
◼ Mafunso onse okhudza madeti ndi malo a misonkhano yachigawo m’maiko ena ayenera kulunjikitsidwa ku maofesi ake a nthambi. Makeyala a maofesi a nthambi padziko lonse amapezeka patsamba lothera mu Yearbook.
◼ Ma Magazine File Case atsopano apulasitiki atsika mtengo wake kuchoka pa K48.00 kukhala K18.00 kuyambira April 1, 1996.
◼ Zofalitsa Zomwe Zilipo:
Knowledge That Leads to Everlasting Life—Chingelezi
Mabaundi voliyumu a Watchtower a 1951, 1952—Chingelezi