Bokosi la Mafunso
◼ Kodi mawuwa “mbale” ndi “mlongo” ngoyenera kugwiritsiridwa ntchito kwa ayani?
Pamene agwiritsiridwa ntchito m’lingaliro lenileni, mawuwa “mbale” ndi “mlongo” amaloza kwa anthu amene ali ndi makolo amodzimodzi. Unansi wachibadwa umenewu nthaŵi zambiri umachititsa kukondana kwakukulu, ndipo chikondi chimene anthu awa amakhala nacho chimalimbitsidwa kwambiri ndi zinthu zonga kakhalidwe kawo, malo, ndi mtima.
Yesu anaphunzitsa ophunzira ake kutcha Yehova “Atate wathu” m’pemphero. Kugwiritsira ntchito mawuwo kumatanthauza kuti monga Akristu, tonsefe tili m’banja logwirizana mmene timasangalala ndi unansi waukulu wauzimu. Zimenezi zinagogomezeredwa kwambiri ndi Yesu pamene anauza otsatira ake kuti “inu nonse muli abale.”—Mat. 6:9; 23:8.
Chifukwa cha unansi wathu wauzimu wogwirizana m’banja la Mulungu, timatchana “Mbale” ndi “Mlongo,” makamaka pamisonkhano ya mpingo. Pazochitika zauzimu zimenezi, amene akutsogolera pamsonkhanopo amadziŵikitsa anthu obatizidwa mwa kugwiritsira ntchito mawu akuti “mbale” kapena “mlongo” otsatiridwa ndi dzina lomaliza la munthu amene akukamba naye.
Bwanji ngati munthu wosabatizidwa akufuna kutengamo mbali m’misonkhano? Pamene munthu wakhala akugwirizana ndi anthu a Yehova kwa nthaŵi yakutiyakuti ndipo ali pafupi kudzipatulira, akumadziyesa iye mwini mmodzi wa Mboni za Yehova, palibe choletsa kugwiritsira ntchito mawuwo “Mbale” kapena “Mlongo” musanatchule dzina lake lomaliza. Zimenezi ziyenera kukhala motere makamaka ngati munthuyo wakhala wofalitsa wosabatizidwa.
Komabe, anthu okondwerera amene angoyamba posachedwapa kupezeka pamisonkhano yathu sanatengebe sitepe imene ingawadziŵikitse kuti ali a m’banja la Mulungu. Anthu ameneŵa sayenera kutchedwa “Mbale” kapena “Mlongo,” popeza alibe unansi wauzimu wa banja la Mulungu. Chotero pamisonkhano, tiyenera kuwaitana mwaulemu kwambiri, tikumagwiritsira ntchito mawu aulemu oyenera onga “A” ndi dzina lawo lomaliza.
Kugwiritsira ntchito mawuwo “mbale” ndi “mlongo” pamisonkhano yathu ya mpingo kumasonyeza unansi wogwirizana kwambiri ndi wamtengo wapatali kuposa uliwonse wosonyezedwa ndi maina oyamba. Kumatikumbutsa za unansi wathu wodalitsika kwambiri umene tili nawo monga banja lauzimu lotsogozedwa ndi Atate mmodziyo, Yehova Mulungu. Timakumbutsidwanso za chikondi chakuya chimene tili nacho kwa wina ndi mnzake.—Aef. 2:19; 1 Pet. 3:8.