Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 8/96 tsamba 2
  • Misonkhano Yautumiki ya August

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Misonkhano Yautumiki ya August
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Timitu
  • Mlungu Woyambira August 5
  • Mlungu Woyambira August 12
  • Mlungu Woyambira August 19
  • Mlungu Woyambira August 26
Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
km 8/96 tsamba 2

Misonkhano Yautumiki ya August

CHIDZIŴITSO: Utumiki Wathu Waufumu udzandandalika Msonkhano Wautumiki wa mlungu uliwonse m’mwezi wa August. Mipingo ingasinthe mofunikira kuti ikapezeke pa Msonkhano Wachigawo wa “Amithenga a Mtendere Waumulungu” ndi kukwanitsa kupenda mfundo zazikulu za programuyo kwa mphindi 30 pa Msonkhano Wautumiki wa mlungu wotsatira. Kupenda programu ya msonkhano wachigawo ya tsiku ndi tsiku kuyenera kugaŵiridwa msonkhano wachigawo usanafike kwa abale aŵiri kapena atatu amene adzakhoza kusumika maganizo pa mfundo zofunikira. Kupenda kokonzekeredwa bwino kumeneku kudzathandiza mpingo kukumbukira mfundo zazikulu zogwiritsira ntchito mwaumwini ndi zogwiritsira ntchito m’munda. Ndemanga za omvetsera ndi zokumana nazo zimene zinasimbidwa ziyenera kukhala zachidule ndi zolunjika.

Mlungu Woyambira August 5

Nyimbo Na. 56

Mph. 10: Zilengezo zapamalopo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu Waufumu.

Mph. 20: “Kulengeza Uthenga Wabwino Mosaleka.” Nkhani ndi kukambitsirana ndi omvetsera. Phatikizanimo mbali za mu Insight on the Scriptures, Voliyumu 2, tsamba 673, ndime 1.

Mph. 15: “Lengezani Uthenga Wabwino wa Ufumu ndi Mabrosha.” (Ndime 1-5) Gwiritsirani ntchito ndime yoyamba m’mawu oyamba. Thirirani ndemanga zolimbikitsa ponena za ubwino wa kugwiritsira ntchito m’munda mabrosha a Moyo pa Dziko Lapansi ndi “Tawonani!” Konzani zitsanzo zinayi zoyesezedwa bwino, zosonyeza mmene maulendo oyamba ndi obwereza angachitidwire ndi mabrosha ameneŵa. Chitani kuti wofalitsa wachichepere, mothandizidwa ndi kholo lake, achite chitsanzo cha maulaliki ndi brosha la Moyo pa Dziko Lapansi. Ofalitsa angafune kupanga maulaliki awo ozikidwa pa awo operekedwa pano pogwiritsira ntchito mabrosha ena.

Nyimbo Na. 136 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira August 12

Nyimbo Na. 192

Mph. 15: Zilengezo zapamalopo. Lipoti la maakaunti. Phatikizanipo ndemanga zolimbikitsa ponena za “Njira Zokhaliramo ndi Mbali,” mu Nsanja ya Olonda ya December 1, 1993, masamba 29-31.

Mph. 15: “Lengezani Uthenga Wabwino ndi Mabrosha.” (Ndime 6-8) Mwachidule fotokozani zimene zili mu brosha la Boma. Chitani zitsanzo za maulaliki operekedwawo a ulendo woyamba ndi ulendo wobwereza. Limbikitsani onse kubwerera kumene anagaŵira zofalitsa.

Mph. 15: “Zopereka ku Ntchito ya Sosaite Yapadziko Lonse Zichirikiza Kufutukuka.” Nkhani yokhudza mtima yoperekedwa ndi mkulu. Phatikizanimo ziŵerengero zina za kupita patsogolo kwa ntchito ya Ufumu m’maiko ena otchulidwawo, monga momwe zalembedwera mu Yearbook.

Nyimbo Na. 9 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira August 19

Nyimbo Na. 174

Mph. 10: Zilengezo zapamalopo. Pendani Bokosi Lamafunso.

Mph. 15: “Kodi Ndani Ali Woyeneretsedwa Kulalikira?” Mkulu akambitsirana nkhaniyo ndi ofalitsa aŵiri kapena atatu. Gogomezerani kuti tikulandira maphunziro abwino koposa amene angapezeke, otikonzekeretsa mokwanira monga atumiki a Mulungu. Tilibe chifukwa chodzionera kukhala wopereŵera kuti tilalikire.

Mph. 20: “Mmene Tingapangire Ophunzira ndi Buku la Chidziŵitso.” Kukambitsirana ndi omvetsera kwa ndime 17-26 za mphatika ya Utumiki Wathu Waufumu wa June 1996. Linganizani pasadakhale kuti mukaphatikizepo zokumana nazo za kumaloko za awo amene akuchititsa maphunziro m’buku la Chidziŵitso. Anene mawu olimbikitsa ponena za mmene agwiritsirira ntchito njira zopezeka m’mphatikayi ndi mmene athandizidwira kuchititsa phunziro la Baibulo lapanyumba lopita patsogolo kwambiri. Limbikitsani onse kusunga mphatikayo ndi kuipenda paumwini nthaŵi zonse pamene ayambitsa phunziro latsopano.

Nyimbo Na. 189 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira August 26

Nyimbo Na. 104

Mph. 10: Zilengezo zapamalopo. Pendani “Programu Yatsopano ya Tsiku la Msonkhano Wapadera.”

Mph. 20: Kukhala ndi Chikondwerero pa Kupita Kusukulu kwa Ana Anu. Nkhani ya mkulu. Pendani chidziŵitso chimene chili m’brosha la Mboni za Yehova ndi Maphunziro, masamba 2-5, mukumasonyeza chifukwa chake timayamikira maphunziro ofunika amene amaperekedwa kusukulu. Kambani za mmene tingafotokozere mochenjera kwa aphunzitsi chifukwa chimene timaikira zonulirapo zauzimu patsogolo pa zinthu zakuthupi. Phatikizanipo mfundo zochokera mu “Mawu Omaliza,” patsamba 31. Limbikitsani makolo kugwiritsira ntchito njira zoperekedwa mu Galamukani! wa September 8, 1988, tsamba 11.

Mph. 15: Pendani Mabuku Ogaŵira mu September. Tidzagwiritsira ntchito buku lakuti Life—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation? Sonyezani kuti bukuli lili ndi nkhani zambiri. Mitu 1-15 imapenda kwambiri za malingaliro osiyana a mmene moyo unakhalirako; mutu 16 umayankha funso lovutitsa anthu onse lakuti, “Kodi Nchifukwa Ninji Mulungu Amalolera Kuvutika?”; mitu 17-18 imalimbikitsa kukhala ndi chikhulupiriro pa Baibulo monga Mawu a Mulungu odalirika ndi ouziridwa; mitu 19-20 imanena za uthenga wabwino wa Ufumu ponena za moyo padziko lapansi mu Paradaiso ndi kufotokoza moupezera. Chitani kuti wofalitsa wokhoza agwiritsire ntchito amodzi a mafikidwe ameneŵa kusonyeza ulaliki wachidule wa buku la Creation. Ngati mpingo ukali ndi makope a Kupangitsa Moyo Wanu wa Banja Kukhala Wachimwemwe kapena Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi mu sitoko, ameneŵa angagaŵiridwe.

Nyimbo Na. 113 ndi pemphero lomaliza.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena