Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu January: Buku lililonse la masamba 192 lofalitsidwa 1984 isanafike limene mpingo ungakhale nalo m’stoko. Mipingo imene ilibe mabuku ameneŵa ingagaŵire Kupulumuka Kuloŵa m’Dziko Lapansi Latsopano. February: Buku lililonse lamasamba 192 limene mpingo ungakhala nalo m’sitoko. March: Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. April: Makope a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!
◼ Ofalitsa obatizidwa onse amene adzapezekapo pa Msonkhano Wautumiki mlungu wa January 6 adzapatsidwa makhadi a Advance Medical Directive/Release ndi ma Identity Card a ana awo.
◼ Kuyambira m’February, ndipo osapyola pa March 2, nkhani yapoyera yatsopano ya woyang’anira dera idzakhala yakuti “Gwiritsirani Ntchito Maphunziro Kutamandira Yehova.”
◼ Mipingo iyenera kupanga makonzedwe oyenera a Chikumbutso chaka chino pa Sande, March 23, dzuŵa litaloŵa. Ngakhale kuti nkhani ingayambe mwamsanga, musayendetse zizindikiro za Chikumbutso kufikira dzuŵa litaloŵa. Funsirani kwa odziŵa nthaŵi pamene dzuŵa limaloŵa kudera kwanuko. Pakuti simudzakhala ndi msonkhano uliwonse tsikulo kusiyapo kukumana kwa utumiki wakumunda, muyenera kupanga makonzedwe oyenera akuchita Phunziro la Nsanja ya Olonda nthaŵi ina. Oyang’anira madera adzafunikira kusintha ndandanda zawo zamisonkhano mlunguwo malinga ndi mikhalidwe ya kumaloko. Ngakhale kuti mpingo uliwonse ungakonde kuchita Chikumbutso paokha, nthaŵi zina sikungatheke kutero. Kumene mipingo ingapo imagwiritsira ntchito Nyumba ya Ufumu imodzi, mwina mpingo umodzi kapena yoposerapo ingakapemphe malo kwina ogwiritsira ntchito madzulowo. Chikumbutso sichiyenera kuyamba mochedwa kwambiri moti nkukhala kovuta kwa atsopano kupezekapo. Ndipo programuyo siiyenera kukhala yopanikiza kwambiri moti nkusoŵa nthaŵi phwandolo lisanachitike kapena pambuyo pake ya kupatsa moni alendo, kupanga makonzedwe akupitiriza kupatsa chithandizo chauzimu kwa okondwerera, kapena kukhala ndi mayanjano olimbikitsana ndi ena. Akulu atapenda mosamalitsa mbali zonse zofunika, ayenera kusankha kuti ndi makonzedwe ati omwe adzathandiza bwino kwambiri awo omwe adzapezekapo pa Chikumbutso kuti apindule mokwanira ndi chochitikacho.
◼ Nkhani yapoyera yapadera ya nyengo ya Chikumbutso cha 1997 idzaperekedwa pa Sande, April 6. Autilaini yake idzaperekedwa. Mipingo imene idzakhala ndi woyang’anira dera, msonkhano wadera, kapena tsiku la msonkhano wapadera kumapeto kwa mlunguwo, idzakhala ndi nkhani yapadera mlungu wotsatira. Palibe mpingo umene uyenera kukhala ndi nkhani yapadera isanafike April 6.
◼ Bungwe la akulu liyenera kudziŵa kuti masinthidwe otsatiraŵa afunikira kutsatiridwa pamene mpingo uli ndi misonkhano yaikulu yakumaloko: Pamene mukhala ndi tsiku la msonkhano wapadera, mpingo uyenera kukhala ndi misonkhano yonse mlunguwo, kusiyapo Msonkhano Wapoyera ndi Phunziro la Nsanja ya Olonda zimene zimachotsedwapo. Pamene mukhala ndi msonkhano wadera, mpingo udzachotsaponso Sukulu Yautumiki Wateokrase ndi Msonkhano Wautumiki; Phunziro la Buku la Mpingo lokha nlimene lidzachitidwa mlunguwo.
◼ Chiwonkhetso cha opezeka pa Misonkhano Yachigawo yonse 13 ya “Amithenga a Mtendere Waumulungu” yochitidwa m’Malaŵi mu 1996 chinali 117,438 ndipo odzipatulira chatsopano okwanira 2,144 anabatizidwa.
◼ Kuyambira tsopano chipinda chamabuku cha Sosaite cha ku Area 11, Plot 36, Lilongwe, chizitsegulidwa pa Lolemba ndi Lachisanu kuyambira 8:00–11:45 a.m. ndi 1:00–4:30 p.m.
◼ Makonzedwe amapangidwa akukumana kwa akulu ndi apainiya okhazikika December iliyonse. Cholinga cha msonkhanowu ndicho kuthandiza ndi kulimbikitsa apainiya mu utumiki wawo. Kodi msonkhano umenewu wachitika kale mumpingo wanu? Ngati simunachite, chonde pangani makonzedwe a kukhala nawo, mwachedwa kale ndi mwezi umodzi.
◼ Zofalitsa Zomwe Zilipo:
Olinganizidwa Kutsiriza Uminisitala Wathu—Chicheŵa
Imbirani Yehova Zitamando (laling’ono)—Chingelezi
Trakiti Na. 22—Chingelezi