Kusamalira Magazini ndi Mabuku Mumpingo
1 Zofalitsa monga ma Baibulo, mabuku, timabuku, magazini ndi matrakiti timazipeza kudzera mumpingo. Kaŵirikaŵiri Sosaite imatumiza zinthu zimenezi ku mpingo pangongole ndiyeno ofalitsa ndi apainiya amaziwombola, ndiyenonso iwo amazigaŵira kwa awo amene amakonda choonadi.
2 Pakali pano, pali kufufuza kumene kukuchitidwa ndi oyang’anira oyendayenda pa maakaunti a mipingo. Malinga ndi malipoti amene talandira pakali pano, mipingo ina ikulimbikira kuwongolera maakaunti ndipo tikuiyamikira mipingo imeneyi. Tikhulupiriranso kuti mipingo yambiri idzaona mvula yabwino yomwe tinali nayo chaka chino kukhala mwaŵi kuti agulitse mbewu zawo ndi kukonza maakaunti awo. Zifukwa zazikulu zimene zimapangitsa maakaunti kuipa m’mipingo yambiri ndizo: “Mabuku otengedwa pangongole ndi ofalitsa”; “Kusasunga zolembedwa zolongosoka”; ndipo “Maakaunti samaŵerengedwa konse.”
3 Tikumalingalira zimenezi, tingafunse mafunso otsatirawa: Kodi kuli bwino kupereka magazini ndi mabuku kwa ofalitsa PANGONGOLE? Kodi abale ogaŵiridwa gawo la kuyang’anira zinthu zimenezi ayenera kusamalira motani mathayo awo? ndipo kodi apainiya ayenera kuwombola mabuku kaamba ka apabanja pa mtengo wa apainiya?
4 Choyamba, kodi mabukuwo ndi ayani? Mosakayikira, ndi a Sosaite ndipo malinga ndi malangizo a Sosaite m’chilengezo chakuti, “Osaperekanso Mabuku Pangongole,” cha mu Utumiki Wathu Waufumu wa April 1994, palibe amene ayenera kupatsidwa mabuku pangongole. Chimodzimodzinso ndi magazini ndi masabusikripishoni. Samatengedwa pangongole. Choncho ngati mkulu kapena mtumiki wotumikira wosamalira mabuku wapereka mabuku pangongole kapena kulola ngongole ya winawake, kodi ndi ngongole kapena kuba? Ndi kuba, chifukwa chakuti palibe mkulu kapena mtumiki wotumikira amene ali ndi ulamuliro wa kuwapereka pangongole. Ndiko kusuliza malangizo ochokera ku Sosaite. (Onani Nsanja ya Olonda ya April 15 1994, masamba 19-21, “Kodi Nkubadi?”) Komabe, makonzedwe ameneŵa asanayambe kugwira ntchito, ofalitsa ena anatenga mabuku pangongole ndipo sanawalipirirebe. Ngati zili choncho, ayenera kuthetsa ngongole yawo ku mpingo mwamsanga pamene iwo angathe kutero.—Salmo 37:21.
5 Atumiki otumikira amene amasamalira mabuku ndi magazini akuchita utumiki wofunika kwambiri. Iwo ali ndi mwaŵi wapadera ndipo motero ayenera kusamala nawo mathayo awo. Abale ogaŵiridwa ntchitoyi ayenera kudziŵa bwino lomwe malangizo a mu Mpambo wa Zofalitsa za Watch Tower (Malangizo) ndi S-AB-27 (Malangizo a Kasungidwe ka Maakaunti a Mpingo), kotero kuti mabuku asaunjikane. Zosoŵa za mpingo ziyenera kudziŵidwa pasadakhale ndipo chilengezo chiyenera kuperekedwa ku mpingo pamene mukufuna kutumiza maoda a mabuku.
6 Apainiya ndi oyang’anira oyendayenda amawombola magazini ndi mabuku okagaŵira pa mtengo wapadera. Zimenezi zimawathandiza kulipirira zowonongedwa zawo za m’munda. Apainiya ndi oyang’anira oyendayenda saloledwa kuwombola mabuku ndi magazini pa mtengo wapadera kaamba ka ofalitsa ena, apabanja kapena mabwenzi. Kumeneku kungakhale kugwiritsira ntchito mwaŵi molakwa ndipo kungaonedwe monga kubera Sosaite. Ofalitsa ayenera kuwombola zinthu zawo ku mpingo pa mtengo wa ofalitsa. Apabanja ndi achibale a apainiya amene saali apainiya ayenera kuwombola zinthu zawo pa mtengo wa ofalitsa. Ngati mpainiya kapena woyang’anira woyendayenda apereka zofalitsa kwa wofalitsa ayenera kumpatsa pa mtengo wa ofalitsa ndipo ayenera kupereka yapamwambayo kwa mtumiki wosamalira maakaunti kuti aitumize ku Sosaite.
7 Awo amene ali ndi mwaŵi wa kusamalira zinthu za mpingo ndi ife tonse amene timagaŵira nawo, tiyenera kukumbukira kufunika kwa kudalirika ndi kukhulupirika m’njira imene timagwiritsirira ntchito “chuma chosalungama.”—Luka 16:9-13.